{"id":4242,"date":"2026-09-19T12:34:42","date_gmt":"2026-09-19T10:34:42","guid":{"rendered":"https:\/\/ny.alislaam.com\/?p=4242"},"modified":"2026-09-19T12:34:42","modified_gmt":"2026-09-19T10:34:42","slug":"nkumano-pakati-pa-tamim-daari-ndi-dajjaal","status":"publish","type":"post","link":"https:\/\/ny.alislaam.com\/?p=4242","title":{"rendered":"Nkumano pakati pa Tamim Daari ndi Dajjaal"},"content":{"rendered":"<p>Mmahadith ambiri, Rasulullah (Swallallahu \u2018alaihi wasallam) adauza anthu za ma fitnah a Dajjaal ndi chisokonezo chomwe adzabweretse padziko lapansi akadzatulukira.<\/p>\n<p>Poyamba, Rasulullah (Swallallahu \u2018alaihi wasallam) sanadziwitsidwe ndi Allah Ta\u2018ala za nthawi yeniyeni yomwe Dajjaal adzaonekere padziko lapansi. Izi zitha kutsimikizika kudzera mu Hadith iyi pomwe Rasulullah (Swallallahu \u2018alaihi wasallam) adafotokoza kuthekera kwa Dajjaal kutulukira mnthawi ya moyo wake kapena pambuyo pa iye. Rasulullah (Swallallahu \u2018alaihi wasallam) adati, \u201cNgati adzabwere ine ndiri moyo, ndiye kuti ndidzathana naye, ndipo ngati adzabwere ine nditamwalira, ndiye kuti munthu aliyense adzayenera kuyesetsa kudzipulumutsa ku ma fitnah ake, ndipo Allah Ta\u2018ala akhale ondiyimilira wanga kudzapulumutsa Msilamu aliyense.\u201d (Saheeh Muslim #2937)<\/p>\n<p>Komabe, Mtumiki (Swalla Allaahu \u2018alayhi wa aalihi wa sallam) asadachoke pa dziko lapansi, Allah Ta\u2019ala adamudziwitsa Rasulullah (Swalla Allaahu \u2018alayhi wa aalihi wa sallam) za malo enieni a Dajjaal komanso nthawi yomwe idzabwere Qiyaamah. Kenako Rasulullah (Swalla Allaahu \u2018alayhi wa aalihi wa sallam) adauza ma Swahaabah (Radhwiyallahu \u2018anhum) kudzera mahadith ambiri kuti kubwera kwa Dajjaal padziko lapansi kudzachitika Qiyaamah isanafike, ndikuti Nabiy Isa (\u2018alaihis salaam) adzatumizidwa kuti akamuphe.<\/p>\n<p>Komanso, Mtumiki (Swalla Allaahu \u2018alayhi wa aalihi wa sallam) asanachoke pa dziko lapansi, Tamim Daari (radhwiyallahu \u2018anhu) adamudziwitsanso Rasulullah (Swalla Allaahu \u2018alayhi wa aalihi wa sallam) za kukumana kwake ndi Dajjaal, ndipo Rasulullah (Swalla Allaahu \u2018alayhi wa aalihi wa sallam) adawadziwitsa ma Swahaabah za kukumana kwake ndi Dajjaal.<\/p>\n<p>Tamim Daari (Radhwiyallahu \u2018anhu) adalowa Chisilamu m\u2019chaka cha chisanu ndi chinayi pambuyo pa hijrah, ndipo Mtumiki (Swalla Allaahu \u2018alayhi wa aalihi wa sallam) adachoka pa dziko lino kumayambiriro kwa chaka chakhumi ndi chimodzi pambuyo pa hijrah.\u00a0 (Siyar A\u2019laamin Nubalaa 2\/442)<\/p>\n<p>Atalowa Chisilamu, Tamim Daari (radhwiyallahu \u2018anhu) anabwera kwa Rasulullah (sallallahu \u2018alaihi wasallam) ndipo anamuuza kuti asanalowe Chisilamu, pamene iye ndi anzake anali paulendo wa panyanja, anakumana ndi chimphepo champhamvu chomwe chinapangitsa kuti sitima yawo ikankhidwe pachilumba china. Pachilumbachi, adamuona Dajjaal, atamangidwa unyolo, ndipo kukambirana komwe kudatenga nthawi yaitali kunayambika pakati pawo ndi Dajjaal.<\/p>\n","protected":false},"excerpt":{"rendered":"<p>Mmahadith ambiri, Rasulullah (Swallallahu \u2018alaihi wasallam) adauza anthu za ma fitnah a Dajjaal ndi chisokonezo chomwe adzabweretse padziko lapansi akadzatulukira. Poyamba, Rasulullah (Swallallahu \u2018alaihi wasallam) sanadziwitsidwe ndi Allah Ta\u2018ala za nthawi yeniyeni yomwe Dajjaal adzaonekere padziko lapansi. Izi zitha kutsimikizika kudzera mu Hadith iyi pomwe Rasulullah (Swallallahu \u2018alaihi wasallam) adafotokoza kuthekera kwa Dajjaal kutulukira mnthawi &hellip;<\/p>\n","protected":false},"author":3,"featured_media":3404,"comment_status":"closed","ping_status":"open","sticky":false,"template":"","format":"standard","meta":{"footnotes":""},"categories":[28],"tags":[],"class_list":["post-4242","post","type-post","status-publish","format-standard","has-post-thumbnail","","category-zizikiro-za-qiyaamah"],"_links":{"self":[{"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=\/wp\/v2\/posts\/4242","targetHints":{"allow":["GET"]}}],"collection":[{"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=\/wp\/v2\/posts"}],"about":[{"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=\/wp\/v2\/types\/post"}],"author":[{"embeddable":true,"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=\/wp\/v2\/users\/3"}],"replies":[{"embeddable":true,"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=%2Fwp%2Fv2%2Fcomments&post=4242"}],"version-history":[{"count":1,"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=\/wp\/v2\/posts\/4242\/revisions"}],"predecessor-version":[{"id":4243,"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=\/wp\/v2\/posts\/4242\/revisions\/4243"}],"wp:featuredmedia":[{"embeddable":true,"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=\/wp\/v2\/media\/3404"}],"wp:attachment":[{"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=%2Fwp%2Fv2%2Fmedia&parent=4242"}],"wp:term":[{"taxonomy":"category","embeddable":true,"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=%2Fwp%2Fv2%2Fcategories&post=4242"},{"taxonomy":"post_tag","embeddable":true,"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=%2Fwp%2Fv2%2Ftags&post=4242"}],"curies":[{"name":"wp","href":"https:\/\/api.w.org\/{rel}","templated":true}]}}