{"id":4262,"date":"2026-10-06T12:22:17","date_gmt":"2026-10-06T10:22:17","guid":{"rendered":"https:\/\/ny.alislaam.com\/?p=4262"},"modified":"2026-10-28T11:41:03","modified_gmt":"2026-10-28T09:41:03","slug":"zopeka-mu-dini","status":"publish","type":"post","link":"https:\/\/ny.alislaam.com\/?p=4262","title":{"rendered":"Zopeka Mu Dini"},"content":{"rendered":"<p>Misampha iwiri ikuluikulu ya shaitaan yosocheretsera munthu ndi chuma ndi akazi. Misampha iwiriyi ndi yowononga kwambiri. Ndipo machimo ambiri omwe amachitika padziko lapansi amachokera ku misampha iwiriyi.<\/p>\n<p>Rasulullah\u00a0 adati &#8220;Ndithudi, dziko lapansi ndi lokoma komanso lokongola ( lokongola komanso lokopa) ndipo Allah Talaa\u00a0 wakusankhani kukhala oimira padziko lapansi, kuti ayang&#8217;ane khalidwe lanu ndi machitidwe anu padziko lapansi. Kotero, samalani ndi fitnah ya dunya ( fitnah ya chuma) ndi fitnah ya akazi, popeza fitnah yoyamba ya Banu Israa&#8217;iil inali fitnah ya &#8220;akazi.&#8221;<\/p>\n<p>Kupatula misampha ya chuma ndi akazi, msampha wina owopsa omwe shaitaan amagwiritsa ntchito kuwononga dini ya anthu ambiri ndi msampha wa bid&#8217;aat (machitidwe atsopano mu deen).<\/p>\n<p><strong>Tchimo limene anthu samapanga Taubah<\/strong><\/p>\n<p>Shaitaan atamva kuti chitseko cha taubah chatsegulidwa kwa Nabi Aadam alaihis salaam ndi ana ake mpaka kumapeto kwa miyoyo yawo, ndipo adazindikira kuti khama la moyo onse losokeretsa munthu &#8216;lidzataidwa mu ngalande&#8217; m&#8217;masekondi ochepa kudzera mwa okhulupirira okhetsa Misozi ya taubah pamaso pa Allah adapanga dongosolo lomwe adzatha kuletsa munthu kupanga taubah.<\/p>\n<p>Shaitaan adati adzalimbikitsa anthu kuchita zinthu za haraam, koma sadzaziona ngati ndi haraam, zomwe sizidzachititse kuti asapange taubah ndikupempha chikhululukiro kwa Allah.<\/p>\n<p>Adzawamiza mu zoipa za bid&#8217;aat (zopeka) ndi zina zotero zomwe adzazikongoletse pamaso pawo, kufikira atayamba kuikira kumbuyo zolakwika zawo. Chifukwa chosaganizira zolakwikazo kukhala machimo, sadzatembenukira kwa Allah kupanga taubah.<\/p>\n<p>Abu Bakr radhwiyallahu anhu akunena kuti Rasulullah swallallahu alaihi wasallam anati &#8220;Gwiritsitsani mwamphamvu kuwerengedwa kwa Laa ilaaha illallah ndi istighfaar (kulapa), ndipo onetsetsani kuti mukuzichita kawirikawiri, pakuti Iblees anati, &#8216;Ndinaononga anthu chifukwa chowaika m&#8217;machimo, ndipo anandiwononga chifukwa chowerenga Laa ilaaha illallah ndikuchita istighfaar.<\/p>\n<p>&#8220;Nditaona zimenezo, ndinawawononga powatangwanitsa m&#8217;zilakolako zawo (Bid&#8217;ah ndi machitidwe ena oipa zomwe amazitenga ngati ndi zolungama). Kotero, amadziona kuti ndi otsogozedwa bwino (ndipo samapanga istighfaar).<\/p>\n<p><strong>Pulani Ya Iblees<\/strong><\/p>\n<p>Imaam Awzaaee rahimahullah akufotokoza kuti Iblees anauza asilikali ake kuti, &#8220;Mudzagwiritsa ntchito yanji poyesa kumusokeretsa munthu?&#8221; Iwo anayankha kuti, &#8220;Tidzagwiritsa ntchito njira zonse zomwe tingathe kuti timupotole!&#8221;<\/p>\n<p>Kenako Iblees anafunsa kuti, &#8220;Kodi mudzatha kuwalepheretsa kuchita istighfaar?&#8221; Iwo anayankha kuti, &#8220;Zimenezo n&#8217;zovuta kwambiri! Zimenezo ndi zomwe zili mgulu la tauheed!&#8221;<\/p>\n<p>Kenako Iblees anaganiza za njira nati, &#8220;Ndithudi ndidzawachititsa machimo ena kukhala ofalikira pakati pawo omwe adzapangitse kusakhala ndi maganizo odzalapa kwa Allah chifukwa chowatenga machimo amenewa ngati oloredwa (.&#8221; Pambuyo pake, Iblees anayamba kuzigwiritsa ntchito zomwe ochitawo poona adazipeputsa chifukwa cha zilakolako zawo.&#8221;<\/p>\n<p>Kuchokera mu Hadith iyi, munthu akumvetsa kuti Qiyaamah isanafike, padzakhala zambiri zosaloredwa zomwe zidzafalale. Anthu adzazitenga kukhala zoloredwa ndipo sadzawaona ngati ndi machimo ndi milandu mu deen.<\/p>\n<p>Kotero, apitiliza kuchita zinthu zimenezi ndipo sadzalapa, chifukwa choziona ngati ndi zinthu wamba kapena miyambo ya anthu.<br \/>\nkujambula zithunzi, akazi akupita kuntchito ndi Pakati pa machimo amenewa pali kusakanikirana kwa amuna ndi akazi, kutenga nawo mbali pochita zinthu momasuka ndi amuna kapena akazi.<\/p>\n<p>Chimodzimodzinso, pali njira zambiri zamalonda zomwe zimati munthu akamaziyang&#8217;anitsitsa ndi kuzilingalira, amazindikira kuti zimafanana ndi mchitidwe wa ribaa, ngakhale kuti zimaperekedwa mwanjira ina. Zonsezi zimakhala gawo la nkhani ya shaitaan.<\/p>\n<p><strong>Ulosi wa Rasulullah Swallallah alaihi wasallam<\/strong><\/p>\n<p>Pokamba za nthawi yomaliza pafupi ndi Qiyaamah, Rasulullah swallallahu alaihi wasallam adaudziwitsanso ummah za nkhani za shaitaan zomwe zikuchitika ndikukhala zenizeni mu ummah wake. Rasulullah adati:<\/p>\n<p>&#8220;E, inu ma Swahaabah anga! Udzakhala bwanji Ummah wanga pamene achinyamata anu adzachimwira poyera, ndipo akazi anu adzapyola malire onse?&#8221; Ma Swahaabah radhwiyallahu anhum adafunsa: &#8220;Kodi nthawi yotero idzabwera ku Ummah?&#8221; Nabiy swallallahu alaihi wasallam adati: &#8220;Inde, ndipo choipitsitsa chidzachirika.&#8221;<\/p>\n<p>Ndipo Nabiy swallallahu alaihi wasallam adati: &#8220;E, ma Sahaabah anga! Udzakhala bwanji Ummah wanga pamene mudzasiye kulamula zabwino ndi kuletsa zoipa?&#8221; Ma Swahaabah radhwiyallahu anhum adafunsa: &#8220;Kodi nthawi yotero idzabwera ku Ummah?&#8221; Nabiy swallallahu alaihi wasallam adati: &#8220;Inde; Ndipo Nabiy swallallahu alaihi wasallam adati: &#8220;E, inu ka Swahaabah anga! Udzakhala bwanji Ummah wanga panthawiyo pamene inu mudzachitenge cholakwa kukhala chabwino ndipo chabwino kukhala cholakwika?&#8221;.<\/p>\n","protected":false},"excerpt":{"rendered":"<p>Misampha iwiri ikuluikulu ya shaitaan yosocheretsera munthu ndi chuma ndi akazi. Misampha iwiriyi ndi yowononga kwambiri. Ndipo machimo ambiri omwe amachitika padziko lapansi amachokera ku misampha iwiriyi. Rasulullah\u00a0 adati &#8220;Ndithudi, dziko lapansi ndi lokoma komanso lokongola ( lokongola komanso lokopa) ndipo Allah Talaa\u00a0 wakusankhani kukhala oimira padziko lapansi, kuti ayang&#8217;ane khalidwe lanu ndi machitidwe anu &hellip;<\/p>\n","protected":false},"author":3,"featured_media":3556,"comment_status":"closed","ping_status":"open","sticky":false,"template":"","format":"standard","meta":{"footnotes":""},"categories":[24],"tags":[],"class_list":["post-4262","post","type-post","status-publish","format-standard","has-post-thumbnail","","category-minda-ya-chikondi"],"_links":{"self":[{"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=\/wp\/v2\/posts\/4262","targetHints":{"allow":["GET"]}}],"collection":[{"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=\/wp\/v2\/posts"}],"about":[{"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=\/wp\/v2\/types\/post"}],"author":[{"embeddable":true,"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=\/wp\/v2\/users\/3"}],"replies":[{"embeddable":true,"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=%2Fwp%2Fv2%2Fcomments&post=4262"}],"version-history":[{"count":5,"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=\/wp\/v2\/posts\/4262\/revisions"}],"predecessor-version":[{"id":4293,"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=\/wp\/v2\/posts\/4262\/revisions\/4293"}],"wp:featuredmedia":[{"embeddable":true,"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=\/wp\/v2\/media\/3556"}],"wp:attachment":[{"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=%2Fwp%2Fv2%2Fmedia&parent=4262"}],"wp:term":[{"taxonomy":"category","embeddable":true,"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=%2Fwp%2Fv2%2Fcategories&post=4262"},{"taxonomy":"post_tag","embeddable":true,"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=%2Fwp%2Fv2%2Ftags&post=4262"}],"curies":[{"name":"wp","href":"https:\/\/api.w.org\/{rel}","templated":true}]}}