Daily Archives: February 12, 2022

Tafseer Ya Surah Alaq

Werenga mdzina la mbuye wako yemwe adalenga (chinachirichonse), adamulenga munthu kuchokera ku dontho la magazi, ndipo mbuye wako ndi olemekezeka, amene adamuphunzitsa munthu kulemba (pogwiritsa ntchito) cholembera, adamuphunzitsa munthu zinthu zomwe zankazidziwa, kotero munthu wapsyola malire chifukwa akudzitenga kuti iye atha kudziimira payekha, ndithudi, kwa mbuye wanu ndiye kobwelera, kodi wamuona uyo (Abu Jahal) amene akuletsa kapolo (Muhammad sallallahu alaih wasallam) akaima kuti apemphere, tandiuza kodi ngati iyeyo (kapolo wanga - Muhammad (sallallah alaih wasallam) ali pa chiongoko kapena akuwalamulira anthu kuchita ntchito zabwino nankha Abu Jahal ali ndi mphamvu zanji kuti amuletse)? Tandiuza ngati iyeyo (Abu Jahal) angakane ndikubwelera m'mbuyo, kodi sakuzindikira kuti Allah Ta’ala akuona zomwe oye akuchhitazo? Sichoncho, ngati sasiya zomwe akuchitazo timukoka tsitsi la paliombo (tiligwira mwamphanvu liombi lake ndikukamponya kumoto. Basi, ayitane gulu lakero ifenso tiitana asilikali athu a kumoto, sichoncho, usamunvere ameneyo oh Muhammad (sallallahu alaih wasallam) (pazimene akukuletsazo, ndipo gwetsa nkhope yako pansi ndipo udziyandikitse kwa mbuye wako.

Read More »