Abdullah bin Abbaas (radhwiyallahu ‘anhuma) adadwala diso zomwe zidapangitsa kuti lidzitulutsa madzi nthawi zonse. Dokotala adamulangiza kuti, “Ndizotheka kuthana nalo vutolo ngati ukufuna kutenga njira zodzitetezera pochita sajdah pa thabwa kwa masiku asanu, osati pansi.”
Abdullah bin Abbaas (radhwiyallahu ‘anhuma) anayankha kuti, “Sindiri okonzeka kuchita zimenezo. Sindingaswali ngakhale rakah imodzi munjira imeneyo. Ndidamva Rasulullah (swallallahu ‘alaihi wasallam) akunena kuti, ‘Munthu amene mwadala samaswalial Swalaah imodzi, adzakumana ndi Allah pa Tsiku la Qiyaamah Allah asali osangalatsidwa naye.’”
Sheikh Moulana Muhammad Zakariyya (rahimahullah) adafotokoza nkhani yomwe ili pamwambapa:
N’kololedwa mwapadera, kuchita Swalaah m’njira yomwe dokotala adalangiza ndipo izi sizingakhale pansi pa chenjezo lomwe latchulidwa mu Hadith. Komabe, Maswahaabah (radhwiyallahu ‘anhum) anali ndi kudzipereka kwakukulu pa Swalaah ndipo chifukwa cha kufunika komwe adawonetsera ku chiphunzitso cha Rasulullah (swallallahu ‘alaihi wasallam), swahaabi Abdullah bin Abbaas (radhwiyallahu ‘anhuma) sanali okonzeka kulandira thandizolo. Ndipotu, maSwahaabah (radhwiyallahu ‘anhum) anali okonzeka kupereka nsembe dziko lonse lapansi chifukwa cha Swalaah imodzi.
(Fazaail-e-A’amaal Tsamba 84)
Alislaam Yeretsani mtima wanu potsatira chisilamu