
Munthu wina anabwera kwa Hazrat Abdullah bin Abbaas (radhwiyallahu ‘anhuma) atalowa i’tikaaf mu Masjid ya Rasulullah (swallallahu alaihi wasallam). Munthuyo anamulonjera ndi salaam kenako anakhala pansi. Hazrat Abdullah bin Abbas (radhwiyallahu ‘anhuma) adati kwa iye:
“Ndikuona kuti ndiiwe okhumudwa.”
Munthuyo anayankha kuti, “Inde, oh msuweni wa Rasulullah (swallallahu alaihi wasallam). (Ndiine okhumudwa chifukwa) ndili ndi ngongole kwa munthu winawake ndipo sindingathe kubweza.”
Hazrat Abdullah bin Abbas (radhwiyallahu ‘anhuma) anafunsa kuti, “Ndilankhule ndi munthuyo m’malo mwako, munthu amene uli naye ngongoleyo (ndi kumupempha kuti akupatse mpata owonjezera nthawi yolipilira ngongoleyo)?”
Munthuyo anayankha kuti, “Ngati mukufuna, mungathe kutero.”
Kenako Hazrat Abdullah bin Abbas (radhwiyallahu ‘anhuma) anatuluka mu mzikiti (kuti apite kwa obwereketsayo ndikulankhula naye m’malo mwa munthuyo).
Munthuyo anamuuza kuti, “Kodi mwayiwala kuti muli mu i’tikaaf?”
Hazrat Abdullah bin Abbas (radhwiyallahu ‘anhuma) anayankha misozi ili m’maso mwake:
“Ayi, sindinaiwale. Komabe, ndinamva munthu amene akugona m’manda awa akunena ( Rasulullah sallallahu alaihi wasallam) — ndipo sipanatenge nthawi yayitali kuyambira pamene ndinamumva akunena izi:
‘Aliyense amene ayenda kuti akwaniritse zosowa za m’bale wake ndikumuchitira zimenezo, ndiye kuti izi ndi zabwino (ndi zopindulitsa kwambiri) kuposa kukhala mu itikaaf kwa zaka khumi; ndipo aliyense amene akhala mu itikaaf kwa tsiku limodzi, ndi cholinga chofuna chisangalalo cha Allah Ta‘ala, ndiye kuti Allah Ta‘ala adzamutalikitsa ndi moto wa Jahannum mtunda wa ngalande zitatu. Ngalande iliyonse idzakhala yayikulu kuposa mtunda wa pakati pa thambo ndi dziko lapansi.’ (Shu’abul Imaan #3679)
Alislaam Yeretsani mtima wanu potsatira chisilamu