Zizindkiro za Qiyaamah

Nkhondo Yaikulu ndi Kugonjetsedwa kwa Istanbul

Mahdi atabwera, Allah Ta‘ala adzawapatsa Asilamu uysogoleri ndi mphamvu padziko lonse lapansi. Akristu adzazindikira kuti Asilamu akupeza thandizo ndipo akukula mphamvu tsiku ndi tsiku. Kenako adzakonza gulu lankhondo lalikulu kuti amenyane ndi Mahdi ndi Asilamu. Zanenedwa mu Hadith kuti Akristu ochokera m’maiko onse adzasonkhanitsa asilikali awo ndikukonzekera kumenyana ndi Asilamu. …

Read More »

Gulu Lankhondo Lokhala ndi Mbendera Zakuda Lochokera ku Khurasaan

Pambuyo poti Mahdi waonekera pakati pa anthu ndipo nkhani ya kuonekera kwake yayamba kufalikira padziko lonse lapansi, gulu lankhondo lokhala ndi mbendera zakuda lidzachoka ku Khurasaan kupita ku Makkah Mukarramah ndikukhalira limodzi ndi Mahdi. Rasulullah (Swallallahu ‘alaihi wasallam) adalimbikitsa ummah kuti udzakhale ndi gulu lankhondo limeneli pobwera kwa Mahdi. Rasulullah …

Read More »

Kuwonekera kwa Nkhani Zikuluzikulu Mahdi Asanafike – Zizindikiro za Qiyaamah

Mahdi (radhiyallahu ‘anhu) asanaonekere padziko lapansi, anthu ambiri padziko lonse lapansi adzakhala Akhristu. (Muslim #2898) M’madera ambiri padziko lapansi, Ummah wa Chisilamu udzakhala ukuvutika ndipo udzazunzidwa ndi kuvutitsidwa ndi makafiri. Nkhondo zambiri zidzabuka ndipo Asilamu padziko lonse lapansi adzakhala akuyembekezera mwachidwi kubwera kwa Mahdi (radhiyallahu ‘anhu) kuti awathandize. Panthawiyo, Sufyaani …

Read More »

Moyo Wa Nabi Issah Alaihis Salaam Akadzabweranso Padziko Lapansi Ndi Kuchuluka Kwa Madalitso Ndi Chitetezo Mnthawi Yake

Nabi Isa (‘alaihis salaam) akadzabwerera padziko lapansi, Mahdi (radhiyallahu ‘anhu) adzakhala mtsogoleri otsogolera Asilamu. Mahdi (radhiyallahu ‘anhu) adzauza Nabi Isa (‘alaihis salaam) kuti atsogolere Asilamu, popeza iye ndi Nabi wa Allah Ta‘ala. (Ibnu Hibbaan #6812, Fitan li-Nu’aim #1028) Asilikali achisilamu, motsogozedwa ndi Nabi Isa (‘alaihis salaam), adzamenyana ndi Dajjaal komanso …

Read More »

Maonekedwe a Nabi Isah ‘alaihis salaam

Nabi Isa (‘alaihis salaam) anatumizidwa ndi Allah Ta‘ala kwa Bani Israa’eel. Limodzi mwa malamulo omwe Allah Ta‘ala adamupatsa linali kupereka uthenga wabwino kwa anthu ake okhudza kubwera kwa Rasulullah (swallallahu ‘alaihi wasallam) padziko lapansi. Allah Ta‘ala akunena mu Qur’aan Majeed: وَ اِذۡ قَالَ عِیۡسَی ابۡنُ  مَرۡیَمَ یٰبَنِیۡۤ اِسۡرَآءِیۡلَ  اِنِّیۡ  رَسُوۡلُ  …

Read More »

Momwe Adabadwira Nabi Isa (‘alaihis salaam)

Dongosolo la Allah Ta‘ala, kukamba momwe amalengedwera anthu, ndilakuti anthu awiri akakumana munthu amapangidwa. Chinthu choyamba ndi kudzera mwa makolo omwe mbewu ya mwamuna imabzalidwa m’mimba mwa mayi. Chinthu chachiwiri ndi mzimu omwe umalowa m’mimba mwa mwana yemwe sanabadweyo akakwanitsa miyezi inayi. Munthu aliyense amene anabwera padziko lapansi adatsatira njira …

Read More »

Nabi Isah ‘alaihis salaaam

Isa (‘alaihis salaam) ndi Mtumiki wa Allah Ta‘ala ndipo ali m’gulu la Aneneri apamwamba. Allah Ta‘ala adamuvumbulutsira Injeel (Baibulo) ndipo adamudaritsa ndi Shari’ah. Iye ndi Nabi amene anatumizidwa padziko lapansi Rasulullah (swallallahu ‘alaihi wasallam) asanabwere. Rasulullah (swallallahu ‘alaihi wasallam) adati, “Ambiyaa onse (‘alaihimus salaam) ali ngati ana a bambo m’modzi. …

Read More »

kupezeka Kwa Chilungamo ndi Madalitso Mkatikati mwa Ulamuliro wa Mahdi (radhwiyallahu ‘anhu)

Ulamuliro wa Mahdi (radhwiyallahu ‘anhu) udzakhala wa chilungamo ndi barakah (madalitso). Popeza Mahdi (radhwiyallahu ‘anhu) adzasankhidwa ndi Allah Ta‘ala kuti autsogolere ummah isadafike Qiyaamah, adzatsogozedwa ndi Allah ndikuthandizidwa ndi Iye. Popeza, chisankho chilichonse chomwe adzachite chidzadzazidwa ndi zabwino ndi chilungamo. Nthawi ya ulamuliro wake, Allah Ta‘ala adzadalitsa Asilamu ndi ma …

Read More »

Mahdi (radhwiyallahu ‘anhu)

Kubwera kwa Mahdi (radhwiyallahu ‘anhu) ndi chizindikiro choyamba mwa zizindikiro zikuluzikulu zomwe zidzawonekere Qiyaamah isadafike. M’mahadith odalitsika ambiri, Rasulullah (swallallahu ‘alaihi wasallam) adalosera za kubwera kwa Mahdi (radhwiyallahu ‘anhu) ku ummah uno. Allaamah Suyuuti (rahimahullah) wafotokoza kuti mahadith okhudzana ndi kubwera kwa Mahdi (radhwiyallahu ‘anhu) ndi ochuluka kwambiri kotero kuti …

Read More »

Momwe Mungadzipulumutsire ku Fitnah (Mayesero)za Dajjaal

M’mahadith odalitsika, Rasulullah (swallallahu ‘alaihi wasallam) adaupatsa ummah mankhwala odzitetezera ku ma Fitna a nthawi zonse komanso Mayesero a Dajjaal. Zanenedwa kuti Olemekezeka Uqbah bin Aamir (radhwiyallahu ‘anhu) nthawi ina adamufunsa Rasulullah (swallallahu ‘alaihi wasallam), “Oh Rasul wa Allah (swallallahu ‘alaihi wasallam)! Kodi njira yopezera chipulumutso ndi iti (kuchokera ku …

Read More »