Dua 1
الْحَمْدُ لِلَّهِ الَّذِي أَحْيَانَا بَعْدَ مَا أَمَاتَنَا وَإِلَيْهِ النُّشُورُ
Kuyamikidwa konse ndi kwa Mulungu Talaa yemwe adatipatsa moyo pambuyo pa imfa ndipo kwa lye yekha ndi kumene tidzabwerere.
Dua 2
الْحَمْدُ لِلَّهِ الَّذِي عَافَانِي فِي جَسَدِي وَرَدَّ عَلَيَّ رُوْحِيْ وَأَذِنَ لِي بِذِكْرِهِ
Kuyamikidwa konse ndi kwa Allah Talaa yemwe wandidalitsa ndi chitonthozo m’thupi langa, nabwezeranso moyo wanga kwa ine, nandilola kuti ndimkumbukire.
Ma Dua Omwe Ndi Sunnah Kuwerenga Ukadzukira Tahajjud
Mukadzukira Tahajjud, werengani ma aya khumi omalizira a Surah Aal-e-Imraan, 397 Komanso werengani izi musanayambe Swala ya Tahajjud:
(1) Allahu Akbar ka 10
(2) Alhamdulillah ka 10
(3) Subhaanallahi wabihamdihi ka 10
(4) Subhaanal Malikil Quddoos ka 10
(5) Astaghfirullah ka 10
(6) Laa ilaaha illallah ka 10
Pambuyo pake werengani dua iyi ka 10:
اللَّهُمَّ إِنِّي أَعُوْذُ بِكَ مِنْ ضِيْقِ الدُّنْيَا وَضِيْقِ يَوْمِ الْقِيَامَةِ
O Allah Talaa ! Ndikupempha chitetezo Chanu ku zopinga zapadziko lapansi ndi zosautsa za tsiku la Qiyaamah.
Mu Hadith ya Sunan Ibni Maajah, zanenedwa kuti Rasulullah (swallahu alayhi wasallam) nayenso ankawerenga dua iyi ka 10:
اللَّهُمَّ اغْفِرْ لِي وَاهْدِنِي وَارْزُقْنِي وَعَافِنِي
Oh Allah Talaa Ndikhululukireni, ndidalitseni ndi chiongoko, ndipatseni riziki ndipo ndipatseni Aafiyah (chitonthozo ndi kufewa).
Alislaam Yeretsani mtima wanu potsatira chisilamu