Mmahadith ambiri, Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wa sallam) adauchenjeza Ummah za Dajjaal ndi mayesero ndi masautso omwe Asilamu adzakumane nawo akadzatulukira padziko lapansi.
Momwemonso, Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wa sallam) adafotokoza momveka bwino momwe Mahdi (radhwiyallahu ‘anhu) ndi Asilamu adzamenyanirane naye pankhondo, ndi momwe Nabiy Isa (‘alaihis salaam) adzamuphere pamapeto pake ku Baab-e-Ludd.
Cholinga chochenjezera motere chinali chakuti Ummah umuzindikire Dajjaal, uzindikire ma fitnah ake, ndi kupewa kugwa m’misampha ndi matchera ake.
Mu Hadith ina, Rasulullah (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wa sallam) adanena kuti Dajjaal sadzatha kulowa malo anayi; (1) Makka Mukarramah, (2) Madinah Munawwarah, (3) Mt Tuur, ndi (4) Musjidul Aqsa. (Musnad Ahmed #23090, 23683)
Kuchokera mmalo anayi onsewa omwe Rasulullah (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wa sallam) adauza Ummah kuti Dajjaal sadzatha kulowa, malo achinayi ndi Musjidul Aqsa. Allah Ta’ala adzasankha malowa kuti akhale likulu la Mahdi (radhwiyallahu ‘anhu) ndi gulu lankhondo la Asilamu pa nthawi yomwe nkhondo ya Dajjaal ndi gulu lake lankhondo idzachitikire.
Chinthu chimodzi chomwe chingalhalenso chifukwa chosankhidwira malowa kukhala malo ogonjetsera Dajjaal, yemwe ndiye gwero la kufr, ndi yakuti Baytul Muqaddas inkatengedwa kuti ndi qiblah ya Ayuda ndi Akristu usadafike nubuwwah ya Rasulullah (swallallahu ‘alaihi wasallam). Ndi chifukwa chake Dajjaal ndi gulu lake lankhondo akadzagonjetsedwera pamenepa, ichi chidzakhala chizindikiro chakuti Chisilamu chapambana chipembedzo chilichonse padziko lapansi, ndipo Chisilamu chidzafalikira padziko lonse lapansi, popeza phata la kufr tsopano lawonongedwa.
M’munsimu muli nkhani yomwe ikufotokoza zambiri za Dajjaal, komanso mkhalidwe ofunikira omwe udzakhalepo padziko lapansi akadzatuluka:
Alislaam Yeretsani mtima wanu potsatira chisilamu