Masunna Ndi Aadaab (Miyambo)

Ubwino Oyendera Odwala 2

Kutalikitsidwa ndi Jahannam kwa ntunda okwana kuyenda zaka makumi asanu ndi awiri (70) Olemekezeka Anas (Radhwiyallahu anhu) akusimba kuti Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) adati: “Amene wapanga wudhu olongosoka (pokwaniritsa masunnah ndi ma mustahabbaat) ndi kupita kukamuona m’silamu nzake yemwe akudwala ndi chiyembekezo choti adzalandire malipiro okayendera nsilamu odwala, munthu oteroyo …

Read More »

Ubwino Oyendera Odwala 1

Kupeza Mwayi Opangiridwa Dua Ndi Angelo Okwana Zikwi Makumi Asanu Ndi Awiri (70,000)  Olemekezeka Ali (Radhwiyallahu anhu) akusimba kuti Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) adati: “Amene amayendera odwala m’bandakucha, angero zikwi makumi asanu ndi awiri (70,000) amamupemphera chifundo kwa Allah mpaka madzulo; Amene angamuyendere odwala madzulo angelo okwana 70,000 amamupemphera chifundo …

Read More »

Kuyendera Odwala

Chipembedzo cha Chisilamu chimalimbikitsa ndi kulamula kuti munthu akwaniritse udindo umene ali nawo kwa Allah ndi udindo umene ali nawo kwa akapolo a Allah. Pankhani ya udindo ndi maufulu omwe munthu ali nawo pa akapolo a Allah, izi zikhoza kugawidwa m’mitundu iwiri ya maufulu. Mtundu oyamba ndi ufulu umene uli …

Read More »

Ma Sunnah Komanso Miyambo Ya Dua 8

20. Musatemberere ana anu pamene mukupempha pa Swalah kapena nthawi ina iliyonse. Ndizotheka kuti temberero lanu litha kukumana ndi nthawi yomwe ma dua amayankhidwa. Olemekezeka Jaabir (Radhwiyallahu anhu) akusimba kuti Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) adati: “Musadzitemberere nokha, ana anu, akapolo anu, kapena chuma chanu.Temberero lanu likhoza kukumana ndi nthawi (yoyankhidwa) …

Read More »

Ma Sunnah Komanso Miyambo Ya Dua 7

18. Popempha mpempheni Mulungu kuti akudalitseni ndi aafiyah (ie kuti akudalitseni momasuka m’magawo onse a moyo wanu). Abbaas (Radhwiyallahu anhu) akusimba kuti: “Nthawi ina ndinamufunsa Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam): “E, Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) wa Allah, ndiphunzitse duwa (yaphindu) imene ndiyenera kupempha kwa Allah. Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) anayankha, “Pemphani …

Read More »

Ma Sunnah Komanso Miyambo Ya Dua 6

16.Lekani kulongosora mwatsatanetsatane pa dua yanu. M’malo mwake, muyenera kupempha zabwino zonse. Nthawi ina Abdullah bin Mughaffal Radhwiyallahu anhu anamva mwana wake akupempha m’mawu otsatirawa: “O Allah! Ndikukupemphani nyumba yachifumu yoyera kumbali yakumanja kwa Jannah ndikalowa m’menemo.” Atamva izi Abdullah bin Mughaffal (Radhwiyallahu anhu) adati: “E, mwana wanga! Mpemphe Allah …

Read More »

Ma Sunnah Komanso Miyambo Ya Dua 5

12. Mukamaliza dua yanu, nenani Aameen. Abu Musabbih Al-Maqraaiy akusimba kuti: Nthawi ina tidakhala pansi ndi Abu Zuhair An-Numairi (Radhwiyallahu anhu) yemwe anali ochokera mwa ma Swahaabah (Radhwiyallahu anhu). Anali odziwa kulankhula. Aliyense mwa ife akamapempha ankati: “Tsindika duayo ndi mawu oti Aamiin, pakuti Amiin ili ngati chidindo papepala. Kenako …

Read More »

Ma Sunnah Komanso Miyambo Ya Dua 4

9. Pamene mukupanga dua, mtima wanu uyenera kukhala olunjika ndi kukhala ndi chidwi kwa Allah, Mtima wanu usakhale osalabadira komanso osaganizira pamene mukupanga dua. Musamamwaze maso kuwayang’ana anthu pamene mukupanga dua. Olemekezeka Abu Hurairah (Radhwiyallahu anhu) akusimba kuti Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) adati: “Pemphani kwa Allah motsimikiza ndi mwachiyembekezo kuti …

Read More »

Ma Sunnah Komanso Miyambo Ya Dua 3

6. Popanga dua, musagwiritse ntchito njira yokayikira. Mwachitsanzo, musanene kuti: “E Allah, ngati Mukufuna kundikwaniritsira zosowa zanga kwaniritsani; Olemekezeka Abu Hurayrah (Radhwiyallahu anhu) adasimba kuti Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam adati; popanga dua m’modzi wa inu asanene kuti Ndichitireni chifundo ngati Mukufuna, ndikhululukireni ngati Mukufuna ndi ndipatseni mariziki ngati mujufuna.’ m’malo …

Read More »

Ma Sunnah Komanso Miyambo Ya Dua 2

2. Popanga dua, kwezani manja anu mofanana ndi pachifuwa chanu (i.e. molingana ndi chifuwa chanu). Olemekezeka Salmaan Faarsi (Radhwiyallahu anhu) akusimba kuti Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) adati: Ndithu Allah ndi olemekezeka, okoma mtima kwambiri komanso owolowa manja. Ulemu Wake ndiwakuti amaona kuti ndi zotsutsana ndi ukulu Wake ndi chifundo Chake …

Read More »