Sahaabah

Kuolowa Manja kwa Olemekezeka Talhah (Radhwiyallahu ‘anhu)

Ali bin Zayd (Rahimahullah) akusimba kuti nthawi ina yake, Nchikumbe wina adapita kwa Talhah (Radhwiyallahu ‘anhu) kuti akapemphe thandizo kwa iye. Nchikumbeyu kudapezeka zoti adali m’bale wake wa Talhah (Radhwiyallahu ‘anhu) ndipo popereka pempho lake, adamupempha kudzera mu ubale omwe udalipo pakati pawo. Talha (Radhwiya Allaahu ‘anhu) adayankha: “Kupatula Inu, …

Read More »

Mantha a Olemekezeka Talha (radhwiyallahu annhu) kuopa kuti Chuma cha Padziko Lapansi chisamuchititse Osakumbukira Allah Ta’ala.

Nthawi ina, Olemekezeka Talha (radhwiyallahu anhu) adalandira ndalama zokwana ma dirham zikwi mazana asanu ndi awiri kuchokera ku Hadhramaut. Kutada usiku, atagona, iye anasowa mtendere, kumangotembenuka kuchoka mbali Ina kupita uku. Poona kukhumudwa kwake, mkazi wake adamufunsa, “Nchiyani chikukuvutitsani, iye adayankha “Kodi munthu angaganize bwanji za Rabb pomwe ali ndi …

Read More »

Olemekezeka Talhah pa Nkhondo ya Uhud

Sayyiduna Zubair bun Awwaam Radhwiyallahu anhu ananena kuti pa nkhondo ya Uhud, Rasulullah swallallahu alaih wasallam adavala zovala zodzitetezera ziwiri mophatikiza. Pankhondoyi, Rasulullah ankafuna kukwera pa thanthwe koma chifukwa cha kulemera kwa zovalazo adalephera kutero. Choncho adamupempha Talhah Radhwiyallahu anhu kuti akhale pansi kuti amuthandizire kuti akwere pa thanthwepo. Talhah …

Read More »

Ulemelero Wapamwamba wa Abu Ubaidah (Radhwiyallahu ‘anhu) Pamaso pa Abu Bakr (Radhwiyallahu ‘anhu)

Rasulullah (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) atamwalira, ma Ansaar adasonkhana ku Saqeefah Bitti Saa’idah m’munda wa zipatso wa Bani Saaidah) kuti asankhe khaleefa pakati pawo. Nthawi imeneyo Abu Bakr ndi Umar anali m’nyumba ya Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) ndipo sankadziwa zomwe zinkachitika. Ali m’nyumbamo, Umar mwadzidzidzi adamva mawu kuitana …

Read More »

Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) Awonetsa ku Ummah Udindo olemekezeka wa Abu Ubaidah (radhiyallahu ‘anhu)

Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) Awonetsa ku Ummah Udindo olemekezeka wa Abu Ubaidah (radhiyallahu ‘anhu) Ranılullah (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) adakhala pamodzi ndi Abu Bakar (Radhwiyallahu ‘anhu), Umar (Radhwiyallahu ‘anhu), Abu Ubaidah (Radhwiyallahu ‘anhu) ndi maSwahaabah (Radhwiyallahu ‘anhum). anapatsidwa chakumwa Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi …

Read More »

Kuopa Allah Taala

Qataadah (Rahimahullah) akusimba kuti Olemekezeka Abu Ubaidah (Radhwiyallahu ‘anhu) ankati, (chifukwa choopa kudzaima pamaso pa Allah Ta’ala pa tsiku la Qiyamah ndi kuwerengetsedwa ntchito zake. وددت أني كنت كبشا، فيذبحني أهلي، فيأكلون لحمي، ويحسون مرقي. “Ndikulakalaka ndikadakhala nkhosa. Ondipha akadandipha, akanadya nyama yanga ndikumwa nsuzi wanga. (Siyaru Aa’laamin Nubalaa 3/14) …

Read More »

Kudzipatula kwa Olemekezeka Abu Ubaidah (Radhwiyallahu ‘anhu) ku Chuma Chadziko Lapansi

Umar (Radhiyallahu ‘anhu) atachoka ku Madina Munawwarah kupita ku Baitul Muqaddas kuti akagonjetse, adayima ku Syria kuti akakumane ndi ma Swahaabah omwe ankakhala kumeneko. MaSwahaabah (Radhwiyallahu ‘anhum) adadzakumana naye (Radhwiya Allahu ‘anhu) yemwe adali kukhala ku Syria ndi kulamulira Syria, adawafunsa: “Ali kuti m’bale wanga?” maSwahaabah (Radhwiyallahu ‘anhu) adafunsa: “Kodi …

Read More »

Chikhulupiliro cha Umar (radhwiyallahu ‘anhu) mwa Abu Ubaidah (radhiyallahu ‘anhu)

Sayyiduna Umar (Radhwiyallahu ‘anhu) adafika kumalire a Shaam (Syria) atauzidwa za mliri omwe udawagwera anthu a ku Syria. Sayyiduna Umar (Radhiya Allaahu ‘anhu) adati: “Ngati imfa ingandifikire Abu ‘Ubaidah bin Jarraah (Radhiya Allaahu ‘anhu) akadali ndi moyo, ndiye kuti ndidzamuika kukhala Khalifa pambuyo panga, ndipo ngati Allah Ta’ala atafuna kundifunsa …

Read More »

Kuwolowa manja ndi Zuhd (Kudzipatula padziko lapansi) kwa Abu Ubaidah (Radhwiyallahu ‘anhu)

Nthawi ina, Umar (Radhwiya Allahu ‘anhu) adatenga ndalama za golide mazana anayi, naziika m’thumba napereka kwa wantchito wake: “Pita kwa Abu Ubaidah (Radhwiyallahu ‘anhu) ndipo ukampatse ndalamazi. Ukakafika kumeneko ukadikire kwa kanthawi kuti ukawone zomwe akachite ndi ndalamazo (ndipo ukabwerere ndikundidziwitsa).” Kapoloyo anatenga thumba la ndalama za golide lija napita …

Read More »