ZAMBIRI ZA IFE

بسم الله الرحمن الرحيم

Allah Ta’ala akufotokoza mu Qur’aan majeed:

الْيَوْمَ أَكْمَلْتُ لَكُمْ دِينَكُمْ وَأَتْمَمْتُ عَلَيْكُمْ نِعْمَتِي وَرَضِيتُ لَكُمُ الْإِسْلَامَ دِينًا

Lero ndakukwaniritsirani chipembedzo chanu ndipo ndakwaniritsa pa inu mtendere wanga. ndakusankhirani chisilamu kukhala chipembedzo chanu. (Surah Maaidah Ayah 3)

Ayah imeneyi idavumbulutsidwa pamwambo wa Hajjatul wadaa (hajj yomaliza ya Nabi (sallallahu alaih wasallam)) mu ayah imeneyi, tadziwitsidwa momveka bwino za Dini yathu – yachisilamu kuti ndi dini yokwanira. Chisilamu ndichipembedzo chokhacho chomwe chizalandilidwe ndikukondedwa ndi Allah Ta’ala ndipo chidzakhalabe choncho mpaka tsiku la Qiyaamah.

M’nyengo iliyonse Allah adasankha akapolo ake osankhika kuti ateteze dini yachisilamu. Anthu amenewa anafalitsa chiphunzitso cha Qur’aan komanso Hadith, kuphazikizapo Aqidah (chikhulupiliro) yolongosoka yachisilamu kwa aliyense.Adafalitsa dini mwakhama yomwe ndiyokwanira kwa anthu onse m’mene inabwelera, monga m’mene masahabah (radhwiyallahu anhum) ma Taabi’in ndi onse amene analowa m’malo mwake adaifalitsira  kwa ummah (m’badwo).

Website imeneyi cholinga chakenso ndichomwecho-kwafikitsira anthu ziphunzitso zoyenera zachisilamu zomwe zidakhazikitsidwa kuchokera m’nthambi zodalilika zadini. Tipemphe Allah kuti alandire nsembe yofooka imeneyi ndikuipanga kukhala njira yoti ummah upindule-ameen.

Tiyenera kuzindikira kuti website imeneyi ikuyenda molangizidwa ndi Muft Ibrahim Salejee (mphuzitsi wankulu ku madrasah a Ta’leemud Deen, ku Durban Ispingo Beach).

Mbiri Ya Muft Ibrahim Salejee (Allah apitilize kwadalitsa)

Muft Ibrahim Salejee adapanga maphunziro awo a Dini ku madrasah otchedwa Darul-uloom Deoband ku India, komanso ndi khalifa (mlowa mmalo) wa Moulana Maseehullah Khan (rahimahullah) aku Jalaalah Baad komanso Muft Mahmood Hassan Gangohi (rahimahullah).

Ku madrasah a Deoband, anadalitsidwa pophunzira pansi pama Ustaadh akuluakulu monga Qaari Tayyib, Muft Mahmood Hassan, Moulana Anzar Shah Kashmeeri (rahimahullah) ndi ena.

Muft Ibrahim Salejee (daamat barakaatuh) Allah adawadalitsanso pogwira ntchito yodalitsika ya tazkiya, (kuunikira anthu m’mene angadziyeretsere muuzimu, zomwe zingapangitse kuti munthu atsatire Dini kwatunthu, kuposera apo, pali maktab (madrasah ang’onoang’ono) ochuluka komanso magawo ena ogwira ntchito yadini omwe akupanga zimenezi molangizidwa ndi Muft saheb.

Anthu ambiri amalumikizana ndi Muft saheb pa nkhani yofuna kutsitsimuka. Amakhala nawo muzochitika ndi ulaliki omwe umapelekedwa sabata iliyonse pamitu yosiyanasiyana monga m’mene angayeretsere mitima yawo ndizina, kudzera mu ulalikiwu amatha kupititsa Imani yawo ndimiyoyo yawo patsogolo.

Atatsiriza kuphunzira, Muft Ibrahim Salejee adabwelera ku South Africa komwe adayambitsa madrasah otchedwa Ta’limud Deen kunyumba kwawo, Alhamdulillah, madrasah amenewa tsiku lalero akutengedwa kuti ndi amodzi mwama madrasah akuluakulu m’dziko la South Africa,anthu ambiri aphunzira pa madrasawa ndikufalitsa Dini dziko lonse lapansi.

Tikupempha Allah kuti awadalitse Muft Saheb powapatsa moyo wautali ndikuti anthu ambiri apitilire kupindula ndi iwowa-ameen.