Minda ya chikondi

Umoyo Wa Chisilamu

Munthu akamira m’madzi n’kumavutika kuti apulumuke, angachite chilichonse kuti apulumutse moyo wake. Ngati Angakwanitse kugwira chingwe chapafupi chomwe angadzitulutse m’madzimo amachikakamira n’kumachiona ngati ndi njira yake yopulumutsira moyo. M’dziko lino lapansi, M’silamu ngati akakumane ndi mafunde amphamvu a fitnah (mayesero) omwe akupereka chiopsezo chommiza m’machimo ndi kuononga chipembedzo chake, adzifunse …

Read More »

Chisilamu Chimaitanira Ku Chiyani?

M’nthawi ya Rasulullah swallallahu alaihi wasallam, anthu osiyanasiyana adayamba kulowa Chisilamu. Uthenga wa Chisilamu ukufalikira ndikufikira madera osiyanasiyana, Aksam bin Saifi rahimahullah mtsogoleri wa banja la Tamiim, adakhala ndi chidwi chofuna kudziwa za Chisilamu. Choncho, adatumiza anthu awiri amtundu wake kuti apite ku Madina Munawwarah kuti akafufuze za Mtumiki swallallahu …

Read More »

Ulaliki Oyamba Nzinda Wa Madinah Munawwarah Pambuyo Pa Nsamuko

Pa nthawi ya nsamuko Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam) atalowa mu mzinda odalitsika wa Madina Munawwarah, anthu ambiri adali kuyembekezera mwachidwi kufika kwake. Ena mwa iwo ndi omwe ankamukonda kwambiri Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam) monga ma Ansaar (radhwiyallahu anhum) a ku Madina Munawwarah komanso Ayuda ndi ena opembedza mafano omwe ankakhala …

Read More »

Mariziq Ali M’manja Mwa Allah Yekha

Cholengedwa chilichonse chimafunikira kudya kuti chipitilire kukhala ndi moyo, ndipo chakudya chili m’manja mwa Allah yekha. Ziyenerezo, mphamvu ndi luntha sizizindikiro zodziwira umoyo wa munthu. Mawu a ndakatulo ndi oonadi: ينال الفتى من عيشه وهو جاهل ويكدى الفتى في دهره وهو عالم ولو كانت الأرزاق تجرى على الحجى هلكن إذا …

Read More »

Allah Ta’ala Yekha Ndi Amene Amadyetsa Zolengedwa Zonse

Tsiku lina, m’nthawi ya Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam) gulu la maswahaaba a fuko la Banu Al-Ash’ar lidayenda kuchokera ku Yemen kupita ku Madina Munawwarah ndi cholinga chopanga hijrah. Atafika ku mzinda odalitsika wa Madinah Munawwarah, adapeza kuti chakudya chawo chomwe adabwera nacho chatha. Choncho adaganiza zotumiza mmodzi mwa maswahaba awo …

Read More »

Mtsutso Wa Pakati Pa Nabi Ebrahim (alaihis salaam) Ndi Namruud

Namrud idali mfumu yopondereza komanso yankhanza imene inkanena kuti iye ndi mulungu ndipo inkalamula anthu kuti adzimulambira. Nabi Ebrahim (alaihis salaam) atapita kwa Namrud ndikumuitanira ku umodzi wa Allah, Namrud chifukwa cha kudzikweza kwake ndi kukakamira kwake, sadavomere ndipo adafunsa Nabi Ebrahim (alaihis salaam) kuti angachite chiyani Mbuye wake. Nabi …

Read More »

Imaam Abu Hanifah Ndi Mafunso Atatu A Mfumu Ya Chiroma

Mfumu yachiroma ulendo wina inatumiza chuma chambiri kwa Khalifa (Mtsogoleri) wa asilamu. isanatumize nthumwi yake ndi chumacho, Mfumuyi inamulamula kuti akafunseko mafunso atatu kwa ma Ulama achisilamu. Nthumwi yachiromayi monga idauzidwira, idafunsa mafunso atatu aja kwa ma Ulama koma sanathe kumupatsa mayankho okhutira. Pa nthawiyo Imaam Abu Hanifah anali mnyamata …

Read More »

Kumudziwa Allah

Allah ndiye Mlengi ndi Mdyetsi wa zolengedwa zonse. Cholengedwa Chilichonse , ngakhale milalang’amba, dzuŵa, nyenyezi, mapulaneti, kapena nthaka ndi zonse zili m’menemo, ndi zolengedwa za Allah. Munthu amene amasinkhasinkha ndi kusakasaka za ukulu ndi kukongola kwa zolengedwa zonsezi angalingalire bwino lomwe ukulu ndi kukongola kwa Amene adazilenga! Allah akutiitanira m’Qur’an …

Read More »