Pamene Allah Ta’ala ankamulamula Rasulullah (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam) kuti anyamuke ulendo wa ku Tabuk, ma Swahaabah ambiri adalibe kalikonse panthawiyo zoti athandizikirw kuyende ulendo wautali ndi wotopetsa, makamaka pamene ankayembekezera kukumana ndi gulu lankhondo lachiroma pankhondo yomwe inali ndi zida zokwanira komanso adalipo ambiri. Choncho pofuna kusonkhanitsa pamodzi ndi …
Read More »Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wa sallam) Kusankha Abdur Rahmaan bin Auf (radhwiya Allahu ‘anhu) kukhala Mtsogoleri wa Asilikali pa nkhondo ya Dumatul Jandal.
M’chaka cha chisanu ndi chimodzi chioangireni Hijrah, m’mwezi wa Sha’baan, Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) adalankhula ndi Abdur Rahmaan bin Auf (Radhwiyallahu ‘anhu) nati kwa iye: “Konzekeretsa ulendo wako, popeza ndikufuna ndikutumize ku ulendo, mwina lero kapena mawa, Insha Allah. M’mawa mwake, Abdur Rahmaan bun Auf (Radhiyallahu ‘anhu) …
Read More »Mantha a Abdur Rahman bin Auf (Radhwiyallahu ‘anhu) kuyankha mlandu ngakhale adawonongera chuma pa ntchito ya Dini.
Shu’bah (Rahimahullah) akuti: Nthawi ina Abdur Rahman bun Auf (Radhwiyallahu ‘anhu) ankasala kudya ndipo nthawi ya iftaar, chakudya chinabweretsedwa kwa iye. Ataona chakudyacho, Abdur Rahman bin Auf (Radhwiyallahu ‘anhu) adati: “Hamzah (Radhwiyallahu ‘anhu) adaphedwa chifukwa cha chikhulupiriro ndipo sitinapeze nsalu yokwanira sanda yake, ndipo anali wabwino kuposa ine. Mus’ab bin …
Read More »Kuwolowa manja kwa Abdur Rahmaan bin Auf (Radhiyallahu ‘anhu)
Miswar bin Makhramah (Radhwiyallahuanhu) akuti: Abdur Rahmaan bun Auf (Radhwiyallahu ‘anhu) nthawi ina adagulitsa munda wa mpesa kwa Uthman (Radhwiyallahu ‘anhu) pamtengo wa ma dinari zikwi makumi anayi (40,000). Abdur Rahmaan (Radhwiya Allaahu ‘anhu) atalandira ndalamazo kuchokera kwa Uthmaan (Radhwiyallahu ‘anhu), nthawi yomweyo adazigawa kwa akazi odalitsika a Mtumiki (Swalla …
Read More »Abdur-Rahman bin Awf (Radhwiyallahu ‘anhu) amatsogolera Swalaah
Paulendo wa Tabuuk, ma Swahaabah (Radhwiyallahu ‘anhum) adali pa ulendo ndi Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam). Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam) adachoka kwa ma Swahaabah (Radhwiyallahu ‘anhum) kuti apite kukazithandiza. Popeza kuti nthawi ya Swalah ya Fajr sidali yochuluka, ndipo ma Swahaabah (Radhwiyallahu ‘anhum) ankaopa kuti nthawi itha kutha, sadamudikire …
Read More »Zizindkiro za Qiyaamah 5
Chikhulupiriro cha Ahlus Sunnah wal Jamaa’ah pa nkhani ya Dajjaal Kutulukira komanso kubwera kwa ma fitnah a Dajjaal zimayendera limodzi m’zitaab za Aqaa’id (Zikhulupiriro za Chisilamu). Ma Ulama a Aqaa’id amavomereza kuti kukhulupirira kutulukira kwa Dajjaal ndi gawo la Aqaa’id ya Ahlus Sunnah wal Jamaa’ah. Mahadith omwe mkati mwake Mtumiki …
Read More »Ubwino Oyendera Odwala 2
Kutalikitsidwa ndi Jahannam kwa ntunda okwana kuyenda zaka makumi asanu ndi awiri (70) Olemekezeka Anas (Radhwiyallahu anhu) akusimba kuti Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) adati: “Amene wapanga wudhu olongosoka (pokwaniritsa masunnah ndi ma mustahabbaat) ndi kupita kukamuona m’silamu nzake yemwe akudwala ndi chiyembekezo choti adzalandire malipiro okayendera nsilamu odwala, munthu oteroyo …
Read More »Olemekezeka Abdur Rahman bin Auf (Radhwiyallahu ‘anhu) ndi mmodzi mwa Asilamu opambana.
Nthawi ina Rasulullah (Swalla-Allaahu ‘alayhi wasallam) adamufunsa Busrah bint Safwan (Radhwiya-Allahu ‘anha) kuti ndi ndani amene ankafuna kukwatira mphwake, Umm Kulthuom bint Uqbah. Adamufotokozera mayina a anthu ochepa omwe adamfunsira mphwakeyo, ndipo adamuwuzanso kuti mwa anthu omwe adamfunsira mphwakeyo ndi Abdur Rahman bin Auf (Radhwiyallahu ‘anhu). Zitatero, Mtumiki (Swalla-Allaahu ‘alayhi …
Read More »Ubwino Osiya Pambuyo Mwana Olungama
Bambo a Nabii Yunus (alayhis salaam) adali munthu Owopa Allah dzina lawo Mattaa. Iwo ndi mkazi wawo kwa nthawi yaitali ankafuna kuti Allah atawadalitsa ndi mwana wamwamuna ndi kumuchita kukhala Mneneri kwa Bani Israeil. Zaka zambiri zidadutsa uku akumapempha mpaka pamapeto pake adaganiza zopita kukasupe odalitsika wa Nabii Ayyoob komwe …
Read More »Olemekezeka Talhah (Radhwiyallahu ‘anhu pa Nkhondo ya Uhud
Pankhani ya kupirira kwa Talha (Radhwiyallahu ‘anhu) pankhondo ya Uhud, Sa’d bin Abi Waqqaas (Radhwiyallahu ‘anhu) adanena izi: Allah Ta’ala amuchitire chifundo Talha. Mosakayikira, mwa ife tonse, adamuthandiza kwambiri Mtumiki (Swallallaahu ‘alayhi wa wasallam) pa tsiku la Uhud. Kenako Sa’d (Radhwiyallahu ‘anhu) adafunsidwa: “Tifotokozere momwe (adamuthandizira kwambiri Mtumiki (Swallallaahu ‘alayhi …
Read More »