Ma Sunnah Ena Onse ndi Aadaab Okhudzana ndi Kudya
1. Musachidandaule kapena kuchipezera vuto chakudya.
Olemekezeka Abu Hurairah radhwiyallahu anhu akunena kuti Rasulullah swallallah alaihi wasallam sanachipezereko vuto chakudya. Ngati akufuna kudya ankadya, ndipo ngati sanachifune ankachisiya (popanda kuchipezera vuto).
2. Musadye chakudya chotentha kwambiri.
Olemekezeka Asmaa bint Abi Bakr radhwiyallahu anhuma akunena kuti nthawi iliyonse akapatsidwa thariid (mtundu wa chakudya), ankamuuza kuti chivundukuridwe kaye mpaka kutentha kuchepe pang’ono. Iye ankati, “Ndinamva Rasulullah swallallahu alaihi wasallam akunena kuti (kudya chakudya chomwe sichotentha kwambiri) ndi gwero lalikulu la madalitso.”
3. Pewani kuononga ndi kupyola malire pa chakudya ndi zakumwa zanu. Allah akunena mu Quraan Majiid kuti,
“Idyani ndi kumwa, ndipo musakhale opyola malire, ndithudi Iye Allah sali opyola malire.
Abdullah bin Amr bin Aas radhwiyallahu anhuma akufotokoza kuti Rasulullah swallallahu alaihi wasallam adati: idyani, imwani ndi kupereka mu njira ya Allah, bola ngati palibe kupyola malire kapena kudzikweza.”
4. Musadye mopitirira muyeso. M’malo mwake, idyani momwe mukufunikira.
Miqdaam radhwiyallahu anhu akusimba kuti Rasulullah swallallahu alaihi wasallam adati:
“Palibe chiwiya chimene munthu angachidzadzitse chomwe chili choipa kuposa m’mimba. Thongo zochepa za chakudya zomwe zingalore nsana kuongoka ( ndikukhala ndi kuthekera kopereka mphamvu zochitira Ibaadah ya Allah) ndi zokwanira kwa munthu. Koma ngati chilakolako chake chopitiliza kudya chili chochuluka ndiye kuti gawo limodzi mwa magawo atatu (lamimba) likhale la chakudya, limodzi likhale la chakumwa, ndi gawo lina likhale la mpweya.”
Alislaam Yeretsani mtima wanu potsatira chisilamu