
Nkhondo ya Badr itafika kumapeto ndipo Rasulullah (swallallahu alaihi wasallam) ndi maswahaabah atapambana, Rasulullah (sallallahu ‘alayhi wasallam) adauza ma swahaabah kuti, “Ndani atapite kukaona momwe Abu Jahl alili?”
Abdullah bin Mas’uud (radhwiyallahu ‘anhu) adapita kukamfunafuna ndipo adapeza kuti ana awiri a ‘Afraa (radhwiyallahu ‘anha) adali atamuvulaza, ndipo anali mu ululu wa imfa.
Abdullah bin Mas’uud (radhwiyallahu ‘anhu) adabwera kwa iye ndipo adaika phazi lake pakhosi pake. Adagwiranso ndevu zake namufunsa kuti, “Kodi ndiwe Abu Jahl? mdani wa Allah! Allah wakunyoza!”
Abu Jahl anayankha kuti, “Kodi pali munthu olemekezeka kuposa ine amene mwamupha?” Anatinso kwa Abdullah bin Mas’uud, “Iwe mbusa wachabechabe! Ukuyesera kukwera phiri lalitali komanso lovuta (ngakhale pa nthawi ya imfa yake, anali odzikweza).”
Pambuyo pake, adati, “Akanakhala wina kupatula mlimi ngati iwe yemwe akanayenera kundipha (kotero kuti zikanakhala cha ulemu kwa ine).”
Abu Jahl adatinso kwa Abdullah bin Mas’uud (radhwiyallahu anhu), “Ukamadula mutu wanga udulire pansi pa khosi langa, pafupi ndi phewa langa, kuti anthu akamauona mutu wanga, ukhale wodabwitsa kwambiri (ndipo ukhale owonekera pamwamba kuposa mitu ya asilikali ena onse omwe aphedwa kuchokera mgulu lathu lankhondo.”
Anamuuzanso Abdullah bin Mas’uud (radhwiyallahu ‘anhu), “Ukabwerera kwa Rasulullah (swallallahu alaihi wasallam), ukamuuze kuti ndinati, “Chidani changa pa iwe lero ndi chachikulu kuposa kale lonse.” Chimodzimodzinso, pa moyo wanga onse, nthawi zonse ndinali mdani wa Allah Ta’ala, koma lero, udani wanga ndi Allah Ta’ala ndi ochuluka kuposa kale lonse.”
Abdullah bin Mas’uud (radhwiyallahu ‘anhu) kenako anamupha pomudula mutu ndi lupanga lake. Kenako anabweretsa mutuwo kwa Rasulullah (swallallahu ‘alaihi wasallam) nati, “Uwu ndi mutu wa mdani wa Allah, Abu Jahl.”
Mtumiki (swallallahu ahu ‘alaihi wasallam) anafunsa mosangalala, “Ndikulumbira mwa Allah (kodi uwu ndi mutu wa Abu Jahl)?” Abdullah bin Mas’uud (radhwiyallahu ‘anhu) analumbira mu dzina la Allah nati, “Uwu ndi mutu wa Abu Jahl, ndipo Allah Ta’ala wandipatsa mphamvu ndi kuthekera komupha.”
Pambuyo pake, Rasulullah (sallallahu ‘alaihi wasallam) anati:
الله أكبر، الحمد الله الذي صدق وعده، ونصر عبده، وهزم الأحزاب وحده
Allah ndiye wamkulu! Kutamandidwa konse ndi kwa Allah Taala! Wakwaniritsa lonjezo Lake, Wathandiza kapolo Wake, ndipo lye Yekha wagonjetsa adani!
Pambuyo pake, Nabiy (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wa sallam) adati kwa Abdullah bin Mas’uud (Radhwiyallahu ‘anhu): “Ndionetse pamene thupi lake lili”
Abdullah bin Mas’uud (Radhiya Allaahu ‘anhu) atamutengera Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wa sallam) kupita naye ku thupi la Abu Jahl, Rasulullah (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wa sallam) adanena mau awa katatu:
الحمد الله الذي أعز الإسلام وأهله
Kutamandidwa konse ndi kwa Allah Taala, Yemwe yekha wapereka ulemu ku Chisilamu ndi anthu asilamu.
Rasulullah (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wa sallam) adati: “Uyu ndi Farawo wa Ummah uno.
Kenako Rasulullah (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wa sallam) adapereka kwa Abdullah bin Mas’uud (radhwiya Allahu ‘anhu) lupanga la Abu Jahl (ngati gawo la chuma cholandidwa).
(Saheeh Bukhaariy #4020, Musnad Ahmad #4247 ndi Fat-hul Baari vol. 7, p. 374)
Alislaam Yeretsani mtima wanu potsatira chisilamu