Nabi Isa (‘alaihis salaam) anatumizidwa ndi Allah Ta‘ala kwa Bani Israa’eel. Limodzi mwa malamulo omwe Allah Ta‘ala adamupatsa linali kupereka uthenga wabwino kwa anthu ake okhudza kubwera kwa Rasulullah (swallallahu ‘alaihi wasallam) padziko lapansi. Allah Ta‘ala akunena mu Qur’aan Majeed:
وَ اِذۡ قَالَ عِیۡسَی ابۡنُ مَرۡیَمَ یٰبَنِیۡۤ اِسۡرَآءِیۡلَ اِنِّیۡ رَسُوۡلُ اللّٰہِ اِلَیۡکُمۡ مُّصَدِّقًا لِّمَا بَیۡنَ یَدَیَّ مِنَ التَّوۡرٰىۃِ وَ مُبَشِّرًۢا بِرَسُوۡلٍ یَّاۡتِیۡ مِنۡۢ بَعۡدِی اسۡمُہٗۤ اَحۡمَدُ ؕ
Ndipo kumbukirani pamene Nabi Isa (‘alaihis salaam), mwana wa Hazrat Maryam (‘alaihas salaam), adati, “Oh ana a Israa’eel! Ine ndiine Mtumiki wa Allah (kutumidwa) kwa inu, ndikutsimikizira Tawrah yomwe (idatumizidwa) m’mbuyomu ine ndisanabwere, ndikulengeza uthenga wabwino wa Mtumiki obwerayo pambuyo panga dzina lake Ahmad (swallallahu ‘alaihi wasallam).” (Surah Saff v. 6)
Nabiy Isa (‘alaihis salaam) adauza anthu ake kuti Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wa sallam) adzatumizidwa kudziko la pansi Qiyaamah,kukhala mthenga omaliza wa Allah Ta’ala, chimodzimodzinso Rasulullah (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wa sallam) adaudziwitsa ummah wake kuti Qiyaamah isanafike, Nabiy Isa (‘alaijh alaih wasallam) adzatumizidwa kwa Dajaal mnthawi ya ummah wake.
Pankhani ya kumufotokoza Nabii Isa (‘alaihis salaam), Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wa sallam) adaudziwitsa Ummah za maonekedwe ake komanso adaudziwitsa Ummah za chovala chomwe adzakhale atavala pamene azidzatsika pansi kuchoka kumwamba.
Rasulullah (Sallallahu ‘alaihi wasallam) anati, “Nabi Isa (‘alaihis salaam) adzatsika kuchokera kumwamba. Kotero, mukadzamuona, zamuzindikireni (ndi kufotokozera komwe ndikukupatsani). Ndi munthu wamtali pang’ono. Khungu lake ndi lokongola komanso lofiirako pang’ono. Adzavala nsalu ziwiri zachikasu ndipo zidzaoneka ngati mutu wake ukukha madzi ngakhale kuti sikudzakhala kunyowa ndi madzi.” (Musnad-e-Ahmad #9270)
Mu Hadith ina, zatchulidwa kuti khungu la Nabi Isa (‘alaihis salaam) lidzakhala lokongola. Khungu lake lidzakhala lofanana ndi mtundu wa tirigu, lokhala ndi mtundu ofiira pang’ono. Adzakhala wamtali pang’ono, okhala ndi chidali chachikulu. Tsitsi lake lidzakhala lalitali, lofika mmapewa ake. Akamadzatsika, adzakhala atavala nsalu ziwiri zachikasu ndipo tsitsi lake lidzaoneka ngati lonyowa.
Chikhulupiliro cha Ahl-e-Kitaab chokhudza kubweranso kwa Nabi Isa (‘alaihis salaam)
Nabi Isa (‘alaihis salaam) akadzatsika kuchokera kumwamba, adzaitanira anthu a zipembedzo zina ku dini ya Chisilamu ndipo adzatsatira Shari’ah ya Rasulullah (swallallahu ‘alaihi wasallam) padziko lapansi. Anthu onse osakhulupilira adzalowa Chisilamu, mpaka sipadzakhala munthu aliyense wokhala padziko lapansi amene sadzakhala Msilamu. Kotero, panthawiyo, chipembedzo chokha padziko lapansi chidzakhala chipembedzo cha Chisilamu.
Mu Qur’aan Majeed, Allah Ta‘ala akuti, “Ndipo sipadzakhala munthu ochokera ku Ahl-e-Kitaab kupatula kuti adzalowa chisilamu kudzera mwa iye (Nabi Isa [alaihis salaam]) asanamwalire (ngati imfa ya Nabi Isa [alaihis salaam]). (Surah Nisaa v. 159)
Mu Hadith yolemekezeka, Rasulullah (sallallahu ‘alaihi wasallam) adanena kuti, “Iye (ngati Nabi Isa [alaihis salaam]) adzawononga mtanda, kupha nkhumba ndikuchotsa jizyah (ngati misonkho yomwe imaperekedwa kwa nzika zosakhala zachisilamu m’dziko la Chisilamu sidzalipidwanso chifukwa aliyense adzalandira Chisilamu). Adzaitanira ku Chisilamu. Kotero, munthawi yake, Allah Ta‘ala adzawononga chipembedzo chilichonse kupatula Chisilamu.” (Musnad Ahmed #9270)
Alislaam Yeretsani mtima wanu potsatira chisilamu