Olemekezeka Waa’il bin Hujr (Radhwiya-Allahu anhu) adali Swahaaba otchuka wa Rasulullah (swallallah alaihi wasallam) yemwe ankachokera dela la Yemen ndipo adali ochokera ku banja lachifumu.
Zanenedwa kuti atanyamuka ku Yemen kubwera ku Madinah Munawwarah kudzalowa Chisilamu, asadafike Rasulullah Allah adawadziwitsa ma Swahaabah kuti watsala pang’ono kufika.
Rasulullah (swallallahu alaihi wasallam) adati kwa ma swahaabah: pali munthu yemwe watsala pang’ono kufika ku Madina Munawwarah kuchokera ku Yemen. Akubwera kuti adzalowe chisilamu ndipo akuchokera ku banja lachifumu ndipo dzina lake ndi Waail bin Hujr.
Atafika, Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam) adamulandira anamulemekeza, ndipo adayala nsalu yake yodalitsika pansi kuti akhalepo. Mtumiki wa Allah (swallallahu alaihi wasallam) adamupemphera duwa yapadera ponena kuti, “O Allah! Dalitsani Waa’il ndi chisomo chanu komanso ana ake ndi zidzukulu zake.” Kenako Mtumiki wa Allah (swallallahu alaihi wasallam) adamusankha kukhala wachiwiri wake kwa anthu aku Yemen.
Asadanyamuke kuchoka ku Madinah Munawwarah, Iye adamupempha Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam) kuti amugaireko malo ku Yemen. Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam) adamupatsa gawo lina la malo kuti lake ndipo adamuuza Mu’awiyah (radhwiyallahu anhu) kuti apite naye limodzi. anamuika ku Yemen kuti akamudulire malowo mdzikolo ndikuwapereka kwa iye.
Kotero, Waail ndi Mu’aawiyah (radhwiyallahu anhuma) ananyamuka limodzi kuchokera ku Madinah Munawwarah. Waa’il (radhwiyallahu anhu) akuyenda pa ngamila, pomwe Mu’aawiyah (Radhwiyallahu anhu), ankayenda pansi. Panthawiyo, Mu’aawiyah (Radhwiyallahu anhu), adali osauka kwambiri kotero kuti adalibe ngakhale nsapato zoti avale paulendowu.
Akuyenda m’chipululu komanso kukutentha, chifukwa chakutentha iye adayamba kumva kuotcha kuphanzi ndipo adayestsa kupikira koma zitavuta, adamupempha Waa’il kuti, “Chonde ndiloleni ndikwele nawo kumbuyo kwanu chifukwa mchenga ukuotcha kuphanzi.”
Waa’il (radhwiyallahu anhu) anayankha kuti, “Siiwe oyenera kukhala malo amodzi ndi munthu ochokera ku banja lachifumu.”
Kenako Mu’aawiyah (Radhwiyallahu anhu) adamupempha kuti chabwino angomubwerekako nsapato zake, koma Waa’il anayankha kuti, “Sindingakubwereke nsapato zanga, koma ngati ukufuna, utha kumayenda mumthunzi wa ngamila yangayi.” Atamva yankho ili, Mu’aawiyah (radhwiyallahu anhu) adakhala chete ndipo anapitiriza kuyenda opanda nsapato.
Atabwerera ku Madinah Munawwarah, Hazrat Mu’aawiyah (radhwiyallahu anhu) adamuuza Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam) za zomwe zinachitika Paulendowu, komanso momwe Waa’il radhwiyallahu anhu adamuchitira.
Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam) adayankha kuti, “Wangolowa kumene Chisilamu, ndi chifukwa chake adakali ndi makhalidwe ena a umbuli omwe anali nawo asanalowe Chisilamu. usazitengere zomwe wakuchitirazo ndipo muzimuchitira zabwino.”
Mukuyankhula kwina, popeza Waa’il adali atangolowa kumene Chisilamu ndipo adangokhala masiku ochepa okha ndi Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) makhalidwe abwino a Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam) anali asanalowe m’moyo wake ndichifukwa chake iye adachita izi. Komabe, pambuyo pake m’moyo wake, adafika pamlingo waukulu pa kudzipereka ndikuonetsa chilungamo.
Kupita kwa nthawi Mu’awiyah (radhwiyallahu anhu) moyo wake udasintha ndipo adasuka mwadzaoneni. Komabe, Allah adalamula kuti nthawi idzafika yomwe adzalamulira dziko lapansi.
Pambuyo pake, Mtumiki wa Allah (mtendere ndi madalitso zikhale pa iye) atamwalira, Hazrat Abu Bakr (Mulungu akondwere naye) adakhala Khalifa, kutsatiridwa ndi Hazrat Umar (Mulungu akondwere naye), Hazrat Uthman (Mulungu akondwere naye), kenako Hazrat Ali (Mulungu akondwere naye).
Pomaliza, nthawi inafika pamene Mu’aawiyah (radhwiyallahu anhu) adasankhidwa kukhala Khalifa wa Asilamu.
Olemekezeka Waa’il atamva za kusankhidwa kwa Mu’awiyah kukhala Khalifa, adanyamuka kupita kukamuona ndikupereka ulemu.
Atamva kuti akubwera, Hazrat Mu’aawiyah adafika kunja kwa mzinda kudzamuchingamira ndi kumulandira. Mu’aawiyah kenako anamupatsa salaam, ndimulemekeza pomukhanzika O afupi ndi naye ndipo anamupatsa mphatso zambiri.
Mu’aawiyah (radhwiyallahu anhu) kenako anamufunsa kuti, “Kodi ukukumbukira tsiku lomwe tinkayenda limodzi?” Waa’il (radhwiyallahu anhu) atakumbukira zomwe zinachitika, ndipo anaona ulemu waukulu ndi kukoma mtima komwe Mu’aawiyah, adamusonyezera, anazimvera chisoni pa khalidwe lake lakale.
Analankhula mumvetsa chisoni pamaso pa Mu’aawiyah ndipo anavomereza kulakwitsa kwake ponena kuti, “Oh Ameerul Mu’mineen! Nthawi imene ija ndinali nditangolowa kumene! Allah watidalitsa ndi Chisilamu. Panthawiyo, sindinkachita zinthu motsatira ziphunzitso za Chisilamu!”
Pambuyo pake, nthawi zonse akamafotokoza nkhaniyi Waa’il ankati, “Nthawi imeneyo, ndikanakonda kuti ndikanamukhanzika kutsogolo kwanga pa chokwera changa!”
Mu nkhaniyi, tikuona kuti ngakhale kuti Hazrat Mu’aawiyah anachitidwa nkhanza zoterezi kuchokera kwa Waa’il (radhwiyallahu anhu) sanaonetse mkwiyo kapena malingaliro alionse oipa mumtima mwake. M’malo mwake, anafika pa mlingoza omelemekeza kwambiri ndi ndi kumuonetsera chikondi ndi kukoma mtima.
Izi zinali chonchi chifukwa chomvera uphungu wa Rasulullah kuti asatengere zolakwika cha Waail (radhwiyallahu anhu) ndipo m’malo mwake apitirizebe kumuchitira zabwino. Iyi inali Sunnah ya Rasulullah (swallallahu alaihi wasallam) kuti nthawi zonse sankazitengera zolakwa za anthu ndipo ankakhululukira omwe ankamulakwira.
Allah atidalitse tonse ndi mphamvu ndi mtima osabweza zoipa za anthu ndikuchita zinthu mogwirizana ndi Sunnah ndi khalidwe lodalitsika la Rasulullah (swallallahualaihi wasallam).
Alislaam Yeretsani mtima wanu potsatira chisilamu