
Nthawi ina, Olemekezeka Zaid bin Thaabit (radhwiyallahu ‘anhu) anayamba kukwera ngamila yake. Abdullah bin Abbaas (radhiyallahu ‘anhuma) atamuona akukwera, adathamanga mwachangu, adagwira zingwe za nyamayo ndikumuthandizira kukwera.
Pofuna kupereka ulemu Abdullah bin Abbaas (radhwiyallahu ‘anhuma), Zaid (radhiyallahu ‘anhu) adamulankhula nati, “Ee msuweni wa Rasulullah (swallallahu alaihi wasallam)! Musachite izi (musagwirizire zingwe za ngamilayi).”
Komabe, Abdullah bin Abbaas (radhwiyallahu ‘anhuma) adapitiliza kugwira chingwecho nati kwa iye, “Umu ndi momwe tidaphunzitsidwira (ndi Rasulullah (sallallahu alaihi wasallam)) kuti tiziyenda ndi ma Ulama athu ndi akuluakulu pakati pathu ( tiyenera kuchita zonse zomwe tingathe kuti tiwalemekeze ndi kuwatumikira).”
Zaid bin Thaabit (radhwiyallahu ‘anhu) kenako anamuuza kuti, “Tambasula dzanja lako.” Abdullah bin Abbaas (radhwiyallahu ‘anhuma) atatambasula dzanja lake kwa iye,Zaid bin Thaabit (radhwiyallahu ‘anhu) anaweramira patsogolo, anagwira dzanja la Abdullah bin Abbaas (radhiyallahu ‘anhuma) nalipsompsona, nati, “Umu ndi momwe tidaphunzitsidwira kuchita zinthu ndi akubanja lolemekezeka la Nabi wathu okondedwa (swallallahu alaihi wasallam).” (Taariikh Ibn Asaakir 19/326)
Kuchokera pa nkhaniyi, tikuona ulemu wapamwamba umene Abdullah bin Abbaas (radhwiyallahu anhuma) adaonetsa kwa Zaid bin Thaabit (radhwiyallahu anhu) popeza anali m’gulu la ma Ulama a ma Sahaabah.
Momwemonso Zaid bin Thaabit (radhwiya Allahu anhu) adamulemekeza Abdullah bin Abbaas (radhwiyallahu anhuma), ngakhale kuti adali ocheperapo msinkhu wake, popeza} Abdullah bin Abbaas (radhwiyallahu anhuma) adali ochokera ku banja lodalitsika la Mtumiki (Rasulullah Allahu alayhi wasallam).
Alislaam Yeretsani mtima wanu potsatira chisilamu