admin

Ma Sunnah Komanso Miyambo Ya Jumu’ah 4

11. Werengani durood mochuluka. Olemekezeka Aws bin Aws radhwiyallahu anhu akufotokoza kuti Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam) adati: “Masiku abwino kwambiri ndi tsiku la Jumuah. 12. Yesetsani kuwerenga duruud chikwi chimodzi (ka 1000) tsiku la Jumuah. Olemekezeka Anas radhwiyallahu anhu akusimba kuti Mtumiki swallallahu alaihi wasallam adati: “Amene amawerenga duruud pa …

Read More »

Kusalilabadira kwa Abu Zar (radhwiyallahu ‘anhu) Ddziko Lapansi

Abu Zar Ghifaari (Radhwiyallahu ‘anhu) anali Sahaabi yemwe ankafanana ndi Nabiy Isa (‘alaihis salaam) m’maonekedwe ake komanso kukongola kwake. Rasulullah (sallallahu ‘alaihi wasallam) anati, “Aliyense amene akufuna kumuona Isa bin Maryam (‘alaihis salaam) Taqwa yake, chilungamo chake, ndi kudzipereka kwake (pa ibaadah), ayenera kumuyang’ana Abu Zar” (Majmauz Zawaaid #15817) Chimodzimodzinso, …

Read More »

Ma Sunnah Komanso Miyambo Ya Jumu’ah 3

9. Ngati n’kotheka, yendani wapansi popita ku musjid kukaswali swalaah ya Jumu’ah. Phanzi lirilonse lomwe mungaponye, mudzalandira mphotho ya kusala kudya kwa chaka chimodzi ndi Tahajjud. Olemekezeka Aws bin Aws Thaqafi radhwiya-Allah anhu akuti, “Ndidamva Rasulullah swallallahu alaihi wasallam akunena kuti, ‘Munthu amene amachita ghusl tsiku la Jumu’ah ndipo amapita …

Read More »

Makolo Kutsogolera Mwa Chitsanzo

Rasulullah swallallahu alaihi wasallam anali olemekezeka kwambiri pa zolengedwa za Allah, Allah adamusankha kukhala Mtumiki Wake omaliza ndipo adamudalitsa ndi dini yolemekezeka kwambiri – dini ya Chisilamu yomwe ndi malamulo abwino kwambiri a moyo kuti munthu atsatire. Munthu akalingalira pa umunthu odalitsika wa Rasulullah swallallahu alaihi wasllam amapeza kuti Allah …

Read More »

Kutsatira kwa Abu Zar (radhiyallahu ‘anhu) Malangizo a Rasulullah (swallallahu ‘alaihi wasallam

Ma’roor bin Suwaid (rahimahullah) akufotokoza izi: Nthawi ina tinadutsa kwa Abu Zar (radhwiyallahu ‘anhu) ku Rabzah ndipo tinaona kuti anali atavala zovala ziwiri. Chimodzi chinali chakale, pomwe china chinali chatsopano, ndipo kapolo wake nayenso anali atavala zovala ziwiri, zomwe chimodzi chinali chatsopano ndipo china chinali chakale. Kenako tidati kwa Abu …

Read More »

Ma Sunnah Komanso Miyambo Ya Jumu’ah 2

8. Pitani mwamsanga ku mzikiti kukaswali Jumu’ah, momwe mungapitire mwamsanga ndi momweso mungalandilire mphotho yochuluka. Olemekezeka Abu Hurairah radhwiya-Allahu ‘anhu akusimba kuti Rasulullah swallallahu alaihi wasallam adati, “Amene amasamba ngati momwe amasambira akakhala ndi janaabah (i.e. amasamba mosamaritsa monga momwe amachitira akakhala ndi janaabah), ndikupita ku Jumu’ah Salaah moyambilira, amalandira …

Read More »

Dua ya Rasulullah (Sallallahu ‘alaihi wasallam) kumupangira Abu Zar (radhwiyallahu ‘anhu)

Abdullah bin Mas’uud (radhwiyallahu ‘anhu) akufotokoza kuti: Rasulullah (Sallallahu ‘alaihi wasallam) atachoka kupita ulendo wa ku nkhondo ya Tabuuk, anthu ena sanapite nawo paulendowo ndipo anasankha kutsala. Ambiri mwa anthuwa anali ma munaafiqiin (achipha maso). Maswahaabah (Radhwiyallahu ‘anhum) akamauza Rasulullah (Sallallahu ‘alaihi wasallam) za anthu omwe anatsala, Rasulullah (Sallallahu ‘alaihi …

Read More »

Ma Sunnah Komanso Miyambo Ya Jumu’ah 1

1. Werengani Surah Dukhaan Lachinayi usiku. Olemekezeka Abu Hurairah (radhwiyallah anhu) akunena kuti Rasulullah (swallallahu alaihi wasallam) adati, munthu amene amawerenga Surah Haa-meem Ad-Dukhaan usiku wa Jumu’ah ( Lachinayi usiku), machimo ake adzakhululukidwa.” 2. Sambani (ghusl) Lachisanu. Munthu amene amasamba Lachisanu, machimo ake ang’onoang’ono amakhululukidwa. Olemekezeka Abu Bakr Siddeeg (radhwiyallahj …

Read More »

Olemekezeka Abu Zar (Radhwiyallahu ‘anhu) Kulemekeza Alendo

‘Isa bin ‘Umailah (Rahimahullah) akufotokoza za munthu wina amene adawona khalidwe la Abu Zar (Radhwiyallahu ‘anhu) kwa anansi ake ndi alendo. Akunena kuti: “Nthawi iliyonse Abu Zar radhwiyallahu anhu akamakama mkaka wa mbuzi zake, poyamba ankagaira mkakawu anthu oyandikana nawo nyunba ndi alendo ake kuti ayambe amwa iwowo kenako ankamwa …

Read More »

Momwe Mungadzipulumutsire ku Fitnah (Mayesero)za Dajjaal

M’mahadith odalitsika, Rasulullah (swallallahu ‘alaihi wasallam) adaupatsa ummah mankhwala odzitetezera ku ma Fitna a nthawi zonse komanso Mayesero a Dajjaal. Zanenedwa kuti Olemekezeka Uqbah bin Aamir (radhwiyallahu ‘anhu) nthawi ina adamufunsa Rasulullah (swallallahu ‘alaihi wasallam), “Oh Rasul wa Allah (swallallahu ‘alaihi wasallam)! Kodi njira yopezera chipulumutso ndi iti (kuchokera ku …

Read More »