Olemekezeka Abdullah bin Abbaas (Radhiya Allaahu ‘anhuma) Amuona Jibreel (‘alaihis ‎swalaam)

Olemekezeka Abdullah bin Abbaas (Radhiya Allaahu ‘anhuma) akusimba kuti nthawi ina iye adali ndi bambo ake pamaso pa Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wa sallam) pomwe Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wa sallam) ankakambirana ndi mumthu wina mwamseri. Popeza kuti Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wa sallam) chidwi chake chonse chidali pa munthuyo, nsana wake udali utalunjika kwa Abbaas (Radhiya Allaahu ´anhuma) ndi mwana wake Abdullah bin Abbaas (radhiya Allaahu ‘anhuma), ndipo mwina Rasulullah (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wa sallam) sadadziwe kuti iwo abwera kudzakumana naye. .

Abbaas (Radhiya Allaahu ‘anhu) adachokapo pamodzi ndi mwana wake ndipo sanapeze mwayi olankhula ndi Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wa sallam). ‎

Atachoka, Abbaas (radhiyallahu ‘anhu) anauza mwana wake Abdullah, “E mwana wanga! Waona momwe msuweni wako ( Rasulullah (sallallahu ‘alaihi wasallam)) wandichitira (mwina samafuna kuyankhula nane)?”

Abdullah (radhiyallahu ‘anhu) anauza abambo ake, “E, bambo anga! Panali munthu wina amene anali ndi Rasulullah (sallallahu ‘alaihi wasallam) amene amalankhula naye (mwina ndi chifukwa chake Rasulullah (sallallahu ‘alaihi wasallam)anakuyang’anitsani nsana).”

Abdullah (radhiyallahu ‘anhu) anati: “Kenako tinabwerera kwa Rasulullah (sallallahu ‎‎‘alayhi wasallam), ndipo bambo anga atakumana ndi Rasulullah (sallallahu ‘alaihi wasallam), anati kwa Iye, “E! Rasulullah (sallallahu ‘alayhi wasallam)! Ndinayankhula zakutizakuti kwa Abdullah (kutanthauza mawu anayankhula aja), ndipo anandiuza kuti ( simunandilabadire popeza) panali munthu amene mumalankhula naye (komabe, sindinathe kumuona munthuyo). Kodi n’zoona kuti mumakambirana zachinsinsi ndi winawake?”

Rasulullah (sallallahu ‘alayhi wasallam) anamufunsa Abdullah (radhiyallahu ‘anhu), “E! Abdullah! Kodi unamuonadi ( munthu amene ndimalankhula naye uja)?” Abdullah anayankha kuti, “Inde (ndinamuona).”

Rasulullah (sallallahu ‘alayhi wasallam) anati, “Amene uja anali Jibreel (‘alayhis salaam). Iye ndi amene ndinatanganidwa naye (kulankhula).”‎ (Musnad Ahmed #2679 ;Majmuz Zawaa’id #15518)

Check Also

Malangizo Otsanzikirana a Rasulullah (swallallahu ‘alaihi wasallam) kwa Mu’aaz (radhwiyallahu ‘anhu) pamene ankamutumiza ku Yemen

Pamene Rasulullah (swallallahu alaihi wasallam) ankatumiza Mu’aaz bin Jabal (radhwiyallahu ‘anhu) ku Yemen kuti akaphunzitse …