Zinthu Zomwe Zimachititsa Kuti Mdalitso Wa Allah Uchoke

Kuipa Kojambula Zithunzi

Tiku lina Rasulullah (swallallahu alaihi wasallam) kulibe ali koyenda, Bibi Aaishah adapachika katani yokhala ndi zithunzi za zinthu zamoyo pakhomo.

Nthawiyo Sayyidah Aaishah (radhwiyallahu anha) sankadziwa kuti zithunzi za zinthu zamoyo zinali zoletsedwa.

Rasulullah (swallallahu alaihi wasallam) atafika kunyumba kwake ndipo maso ake anagwera pa katanilo anakwiya kwambiri. Aaishah anamulonjera, koma Iye sanayankhe moni wake ndipo nthawi yomweyo anapita pa nsaluyo ndikuing’amba.

Ataona momwe wachitira Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wa sallam) Aaishah (radhwiyallahu anha) adazindikira kuti walakwitsa kwambiri, zomwe zachititsa kuti Mtumiki wa Allah asakondwere naye.

Modzichepetsa ndi kulapa kwakukulu, Adati: “Eh Mtumiki wa Allah (swallallahu alaihiwasallam)! Ndikutembenukira kwa Allah kulapa pa tchimo limene ndachita.

Mtima wa Aaishah (radhwiyallahu anha) udali odzazidwa ndi chikondi cha Allah Ta‘ala ndi Mtumiki Wake kotero kuti sakanatha kupirira kuipidwa kwawo ngakhale kwa mphindi imodzi. Choncho, ngakhale kuti sankadziwa za tchimo lomwe adachita, adathamangira kupanga taubah ndipo kenako adamupempha Mtumiki (swallallah alaihi wasallam) kuti amufotokozere tchimo limene anachita kuti asadzabwerezenso mtsogolo.

Rasulullah (swallallahu alaihi wasallam) kenako adamufotokozera zotsatira kuipa kwa tchimo lomwe anachita lopanga zithunzi. Rasulullah adati, “Eh Aaishah! Ndithudi anthu omwe amatenga gawo kujambula zithunzi za zinthu zamoyo adzalandira chilango choipa kwambiri Tsiku la Qiyaamah.”

Tikuyenera kukumbukira kuti monga ziliri kuti kupanga zithunzi za zinthu zamoyo ndi haraam, momwemonso kusunga zithunzi zotere sikukuloledwa. Jaabir (radhwiyallahu anhu) akusimba kuti Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) adaletsa kusunga zithunzi za zinthu zamoyo m’nyumba, komanso kupanga zithunzi zotere.

Opanga Zithunzi Alkulandira Chilango Chachikulu Kwambiri Patsiku la Qiyaamah

Kuopsa kwa tchimo lojambula zithunzi tingakumvetse mu Hadith yomwe Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) adanena kuti mwa amene adzapatsidwe chilango chokhwima pa tsiku la Qiyaamah ndi awa anthu atatu amene amapha Mneneri wa Allah kapena kuphedwa ndi Mtumiki wa Allah, Mtsogoleri yemwe amasocheretsa anthu ake ndi amene amatenga nawo gawo kujambula zithunzi za zinthu zamoyo.

Tangoganizirani momwe tchimo lojambula zithunzi lilili kuopsya kwake kufikira Rasulullah (Swallallahu alaihi wasallam) adatchula opanga zithunzi limodzi ndi amene wapha Nabi wa Allah Talaa kapena mtsogoleri wa mtundu mwe osokeretsa anthu ake!

Mu Hadith ina, kunanenedwa kuti Rasulullah (Swallallahu alaihi wasallam) adati ojambula zithunzi aliyense adzakhala ku moto wa Jahannum, Mu Hadith ina, Rasulullah (Swallallahu alaihi wasallam) adati, “Angelo salowa m’nyumba momwe muli zithunzi (za zinthu zamoyo). ”

Cholengedwa cha ku Jahannum chomwe Chidzalange Anthu Opanga Zithunzi

Mu Hadith ya Sunan Tirmiziy zalemba kuti pa tsiku la Qiyaamah udzaoneka mutu wa cholengedwa china ukutuluka kumoto wa Jahannum, Chidzakhala ndi maso awiri amene chizidzaonera, makutu awiri amene chizidzamvera, ndi lilime limene chizidzalankhulira, chidzati: ndalamulidwa kulanga magulu atatu a anthu opondereza aliyense amene ankaswa malamulo a Allah ” aliyense amene ankapempha kwa milungu ina osati Allah ndi onse ojambula zithunzi za zinthu zamoyo.”

Rasulullah swallallahu alaihi wasallam Salowa mu Ka’bah Sharif chifukwa cha Kupezeka Mafano Mkati Mwake

Nthawi yomwe Makkah inagonjetsedwa ndi asilamu, Rasulullah swallallahu alaihi wasallam anafuna kulowa mu Ka’bah Sharif, koma anabwelera m’mbuyo chifukwa cha mafano omwe anali m’menemo.

Choncho, Mtumiki swallallahu alaihi wasallam adalamula choyamba kuti mafanowo achotsedwe mu Kaaba, ndipo pambuyo pake adalowa la Ka’bah.

Atalowa mu Ka’bah Sharif, Mtumiki swallallahu alaihi wasallam adawona zojambula za zinthu zamoyo m’makoma a Ka’bah Sharif. Mtumiki swallallahu alaihi wasallam anatemberera onse omwe adatenga nawo gawo kujambula zithunzizi ndipo pambuyo pake adalamula kuti zojambulazo zifafanizidwe.

Kumanidwa Barakah ndi Kupezeka kwa Angelo

Masiku ano, chimodzi mwa zifukwa zikuluzikulu zomwe zimapangitsa kuti nyumba za Asilamu zisakhale ndi barakah komanso zopanda madalitso ndichakuti m’nyumba muli zinthu zosiyanasiyana zomwe zili ndi zithunzi za zinthu zamoyo.

Chifukwa cha zithunzizi, angelo achifundo samalowa m’nyumba, ndipo nyumba zotere sizimakhala ndi mtendere ndi madalitso a Allah Talaa.

Chifukwa cha machimo omwe amachitika m’nyumba zotere, anthu okhala m’nyumba zimenezi amakumana mavuto monga kusamvana, kusasangalala komanso kusagwirizana.

Munthu akafufuza chomwe chimayambitsa kuchepekera kwa dini, kapena kusweka kwa maukwati ambiri, kapena kuchita machimo omwe amachitidwa kudzera m’ma social media, ndiye kuti munthu adzazindikira kuti mavutowa akugwirizana ndi kuipa kwa kujambula zithunzi.

Choncho, njira yokhayo yokonza ubale wathu ndi Allah Talaa ndi kubweretsa ubwino mu dini yathu ndi kuti titsatire chiphunzitso cha Mtumiki Swallallahu alaihi wasallam ndi kupewa mitundu yonse yokhudza kujambula.

Tipemphe Allah Talaa kuti azitidalitsa ndi tawfeeq yosunga malamulo a shariah ndi kutsatira Sunnah za Mtumiki Swallallahu alaihi wasallam mbali zonse za moyo wathu.

Check Also

Imaam Ahmad bin Hambal (rahimahulla) Kupindura kuchoka kwa Bishr Haafi (rahimahulla)

Nkhani yotsatirayi ikuunikira kumvetsetsa kwakuya kwa dini ndi ma’rifat (kuzindikirika) ya Allah Talaa zomwe Allah …