
Mu’aaz bin Jabal (radhwiyallahu ‘anhu) akunena kuti, “Nthawi ina, ndinali nditakhala kumbuyo kwa Rasulullah (sallallahu ‘alaihi wasallam) pa bulu pamene naye analinso pomwepo. Panalibe chilichonse pakati pa ine ndi Rasulullah (swallallahu ‘alaihi wasallam) kupatula thabwa la chokhalira (chomwe chimalekanitsa okwera ndi munthu amene wakhala kumbuyo kwake).
“Rasulullah (swallallahu alaihi wasallam) anandilankhula nati, ‘O Mu’aaz!’ Ndinayankha kuti, ‘Ndilipo komanso ndiine okonzeka kukutumikirani O Rasul wa Allah (swallallahu alaihi wasallam).’
“Rasulullah (swallallahu alaihi wasallam) adakhala chete ndipo anapitiriza kukwera nyamayo. Patapita kanthawi, Rasulullah (swallallahu alaihi wasallam) anandiyankhulanso nati, ‘E Mu’aaz!’ Ine ndinayankha nati, ‘Ndilipo ndipo ndi ine okonzeka kukutumikirani E Rasul wa Allah (swallallahu ‘alaihi wasallam).’
“Patapita kanthawi, Rasulullah (swallallahu alaihi wasallam) anandiyankhula kachitatu nati, ‘E Mu’aaz!’ Ine ndinayankha nati, ‘Ndilipo ndiine okonzeka kukutumikirani E Rasul wa Allah (swallallahu ‘alaihi wasallam).’
“Rasulullah (swallallahu ‘alaihi wasallam) anandifunsa kuti, ‘Kodi ukudziwa ufulu wa Allah Ta’ala pa akapolo Ake?’
“Ndinayankha nati, ‘Allah ndi Rasul Wake (swallallahu ‘alaihi wasallam) akudziwa bwino (kutanthauza kuti sindikudziwa).’
“Mtumiki (swallallahu ‘alaihi wasallam) anati, ‘Ufulu wa Allah Ta’ala pa akapolo Ake ndi wakuti azimulambira popanda kumuphatikiza ndi zina ( ayenera kuchita zinthu zonse zomulambira ndi cholinga chomusangalatsa iye yekha ndipo ayenera kukhala omumvera nthawi zonse ndi kupewa kusamumvera Kwake).’
“Pambuyo pake, Mtumiki (swallallahu ‘alaihi wasallam) anapitiriza kukwera nyamayo ndipo anakhala chete kwa kanthawi. Patapita kanthawi kochepa, Rasulullah (swallallahu ‘alaihi wasallam) anandiitananso nati, ‘Ewe Mu’aaz!’ Ine ndinayankha, ‘Ndilipo ndiine okonzeka kukutumikirani, E Rasul wa Allah (swallallahu ‘alaihi wasallam).’
“Rasulullah (swallallahu ‘alaihi wasallam) kenako anandifunsa kuti, ‘Kodi ukudziwa ufulu wa atumiki kwa Allah Ta’ala ngati akwaniritsa zomwe Iye wawalamula kuti achite (ngati ufulu wa atumiki kwa Allah Ta’ala ngati akuchita zinthu zonse zomulambira ndi cholinga chomusangalatsa iye yekha ndikupitirizabe kumumvera nthawi zonse ndi kupewa kusamumvera Kwake)?’
“Ndinayankha kuti, ‘Allah ndi Rasul Wake (swallallahu ‘alaihi wasallam) akudziwa bwino (sindikudziwa).’
“Rasulullah (swallallahu ‘alaihi wasallam) kenako anandiuza kuti, ‘Ufulu wa atumiki kwa Allah Ta’ala ndi wakuti Allah Ta’ala sangawalange ndipo Iye amawalowetsa mu Jannah ( ngati akapolowo apitirizabe kumumvera Allah Ta’ala nthawi zonse ndi kupewa kusamvera Kwake, Allah Ta’ala sadzalanga atumiki Ake powalowetsa ku Jahannum koma adzawadalitsa ndi chifundo Chake ndikuwalowetsa ku Jannah).’”
Kuchokera pa mnkhaniyi, tikuona ubale wapafupi umene Mu’aaz bin Jabal (radhwiyallahu ‘anhu) anali nawo ndi Rasulullah (swallallahu alaihi wasallam).
Chifukwa chomwe Rasulullah (swallallahu ‘alaihi wasallam) adakhalira chete katatu atalankhula ndi Muaaz (radhwiyallahu ‘anhu) kunali kuti akhanzikitse chidwi ndi khumbo mkati mwake lofuna kumvetsera zomwe Rasulullah (swallallahu ‘alaihi wasallam) ankafuna kumuphunzitsa. Popeza kuti nkhani yomwe Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wa sallam) ankafuna kuti amuphunzitse inali yofunikira kwambiri komanso yaphindu, Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wa sallam) adatenga njira imeneyi polankhula naye.
Taonanso ulemu waukulu umene Muaz (Radhwiyallahu ‘anhu) adauonetsa kwa Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wa sallam) polankhula naye.
Muaaz (Radhwiyallahu ‘anhu) adamuyankha Rasulullah (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) mwa mphamvu ndi changu chonchi ma ulendo onse atatu omwe Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wa sallam) adalankhula naye.
(Saheeh Bukhaari #6500, Saheeh Muslim #30, Fathul Baari 11/339)
Alislaam Yeretsani mtima wanu potsatira chisilamu