Kachitidwe ka Mu’aaz (radhiyallahu ‘anhu) Kuwerenga Quraan Majeed pa Tahajjud

Mtumiki (swallallahu ‘alaihi wasallam) anatumiza Mu’aaz (radhwiyallahu ‘anhu) kuti akalamulire gawo lina la Yemen, ndipo Abu Musa Ash’ari (radhwiyalllahu ‘anhu) akalamulire gawo lina.

Mtumiki (swallallahu ‘alaihi wasallam) anawalankhula ndipo anawapatsa uphungu otsatirawu asanawatumize. Anawauza kuti, “Fewetsani zinthu (kwa anthu), ndipo musawakhwimitsire. Perekani uthenga wabwino (kwa anthu), ndipo musawathamangitse (ku dini).”

Mtumiki (swallallahu ‘alayhi wasallam) adatumiza Abu Musa Ash’ari (radhwiyallahu ‘anhu) ku Yemen, ndipo pambuyo pake adatumiza Mu’aaz (radhwiyallahu ‘anhu) ku Yemen.

Akukhala ku Yemen, ma Swahaaba awiriwa ankabwera kudzacheza, makamaka akamayenderana m’madera omwe anali.

Nthawi ina, Mu’aaz bin Jabal (radhwiyallahu anhu) ankadutsa m’dera la Abu Musa Ash’ari (radhwiyallahu ‘anhu), adayima kuti akumane naye. Atakumana, onse awiri adakhala pansi ndikuyamba kukambirana za ndondomeko zawo za tsiku ndi tsiku zowerenga Quraan Majid.

Mu’aaz bin Jabal (radhwiyallahu ‘anhu) adamufunsa Abu Musa Ash’ari (radhwiyallahu ‘anhu), “Oh Abdullah (Abu Musa), kodi ndondomeko yako ya tsiku ndi tsiku ndi yotani pankhani yowerenga Quraan?”

Iye anayankha kuti, “Nthawi iliyonse imene ndingaipeze kuti ndiwerenge Quraan (usiku ndi usana), ndimawerenga).”

Abu Musa (radhwiyallahu ‘anhu) adafunsa Mu’aaz (radhwiyallahu ‘anhu), “nanga ndondomeko yako ndi yotani?”

Mu’aaz (radhwiyallahu ‘anhu) anayankha kuti, “Ndimagona gawo loyamba la usiku, kenako ndimadzuka (kuti ndiwerenge Quraan) nditamaliza kugona kwa nthawi yomwe ndimafunikira kutero. Kenako ndimawerenga Quran kuchuluka kulikonse komwe Allah wandikonzera kuti ndiwerenge (panthawiyo). Ndiri ndi chiyembekezo chodzalandira mphotho kuchokera kwa Allah chifukwa choyimirira pa salaah (usiku ndikuwerenga Quraan), momwemonso, ndili ndi chiyembekezo chodzalandira mphotho kuchokera kwa Allah chifukwa cha kugona kwanga (usiku,motengera ndi momwe tulo langa lilili kuti ndipeze mphamvu zochitira ibaadat kwa Allah Ta’ala masana ndi usiku).”

Check Also

Makhalidwe Abwino a Muaaz bin Jabal (radhwiyallahu ‘anhu)

Farwah bin Nawfal akufotokoza kuti nthawi ina yake, Abdullah bin Masud (radhwiyallahu anhu) adalankhula za …