Pamene Rasulullah (swallallahu alaihi wasallam) ankatumiza Mu’aaz bin Jabal (radhwiyallahu ‘anhu) ku Yemen kuti akaphunzitse anthu dini ndikuwalamulira, posiyana naye, Rasulullah (swallallahu ‘alaihi wasallam) ankayenda naye mpaka kunja kwa mzinda wa Madinah Munawwarah pamene ankamupatsa uphungu osiyanirana.
Rasulullah (swallallahu alaihi wasallam) anamulamula kuti achite zinthu zina zabwino, ndipo anamulamula kuti asamachite zinthu zina. Rasulullah (swallallahu ‘alaihi wasallam) anamuuza kuti:
“Oh Mu’aaz! Ndikukulangiza monga momwe m’bale owona mtima komanso wachifundo amalangizira m’bale wake. Ndikukulangiza kuti nthawi zonse uziopa Allah, uzinena zoona, uzikwaniritsa malonjezo ako, uzisamaritsa zomwe wapatsidwa, uzipewa chinyengo, uzichitira chifundo ana amasiye, uziteteza ufulu wa mnansi, uziubweza mkwiyo wako, uzidzichepetsa nthawi zonse, uzipereka salamu (kwa omwe umakumana nawo), uzilankhula mwaulemu, uzitsatira bwino Qur’an, uziganizira mozama Qur’an (ndi kuitsatira molondola), uzikhala ndi chikondi cha Tsiku Lomaliza (mkati mwa mtima wako), uziopa kudzayankha (pamaso pa Allah pa Tsiku la Qiyaamah), usamakhale ndi ziyembekezo ndi zilakolako zapadziko lapansi, komanso uziwonjezera kuchita zabwino.”
Rasulullah (swallallahu alaihi wasallam) nayenso anamuuza kuti, “Ndikukuletsa kunyoza Msilamu, kunama, kukhulupirira mfundo za wabodza, komanso kusamvera mtsogoleri olungama amene waikidwa pa inu (nthawi iliyonse m’moyo wako, ngati wina wasankhidwa ndi khalifah, ndiye kuti muyenera kumumvera).
“Oh Mu’aaz! Kumbukira Allah pa mwala ulionse ndi mtengo ulionse (ukanayenda padziko lapansi, mukadutsa mwala kapena mtengo, nthawi zonse kumbukirani Allah Ta’ala). Ngati wachita tchimo (chifukwa cha kufooka kwaumunthu), nthawi yomweyo konza pochita tawbah. Ngati tchimolo lachitika mwachinsinsi, pangaso tawbah mwachinsinsi, ndipo ngati tchimolo lachitika poyera, pangaso tawbah poyera.”
Rasulullah (swallallahu alaihi wasallam) adaonjezera kuti, “Nthawi zonse yendera odwala, fulumira kukwaniritsa zosowa za akazi amasiye ndi Asilamu ofooka, khala ndi anthu osauka ndi osowa, chitira anthu chilungamo ngakhale zitakhala zokhudzana ndi inu nokha (ngakhale zitakhala zokhudzana ndi ufulu wako), nthawi zonse lankhula zoona, ndipo pachifukwa cha Allah, musadandaule ndi kutsutsidwa ndi munthu aliyense.” (Hilyatul Awliyaa 1/240)
Malinga ndi nkhani ina, asanapereke Mu’aaz (radhwiyallahu ‘anhu) moni, Nabi (swallallahu alaihi wasallam) adamuuza kuti, “Mwina siudzandionanso kutsogolo (mwanjira ina, uwu ndi mkumano wathu omaliza). Mwina (ukadzabwerera ku Madina,) udzadutsa pafupi ndi musjid yanga kapena manda anga.”
Mu’aaz (radhwiyallahu ‘anhu) anamvetsa izi ngati chizindikiro chomveka bwino chakuti Rasulullah (swallallahu alaihi wasallam) amwalira ndipo sipadzakhalanso mwayi wina oti owobsna ndi kukumana ndi Rasulullah (swallallahu alaihi wasallam) pambuyo pa izi. Atamva izi, Mu’aaz (radhwiyallahu anhu) anayamba kulira chifukwa cha chisoni atasiyana ndi Rasulullah (swallallahu alaihi wasallam).
Rasulullah (swallallahu alaihi wasallam) sanafune kuyang’ana nkhope yake pamene ankalira, kotero anayang’anitsa nkhope yake yodalitsika ku Madinah Munawwarah. Rasulullah (swallallahu alaihi wasallam) kenako anamutonthoza nati, “Ndithudi, anthu omwe ali pafupi nane ndi
omwe ali ndi taqwa (ndiko kuopa Mulungu m’miyoyo yawo), kulikonse kumene ali.” (Musnad Ahmad #22052).
Mu kuyankhula kwina, Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wa sallam) adamufotokozera kuti ngati usunga taqwa ndi sunnah yanga, ndiye kuti udzakhala kutali ndi ine kudziko lina, udzakhala pafupi ndi ine. M’malo mwake, ngati mukhala pafupi ndi ine (monga ku Madinah Munawwarah), koma osakhala ndi taqwa ndi sunnah m’moyo wako, ndiye kuti ngakhale ukukhala mondiyandikira kuthupi, ndithudi, uli patali ndi ine.
Alislaam Yeretsani mtima wanu potsatira chisilamu