
Olemekezeka Abdullah bin Abbaas (radhwiyallahu ‘anhuma) akuti:
Mtumiki wa Allah (swallallahu ‘alaihi wasallam) atamwalira, ndinauza mnzanga wina wachi Ansaari kuti, “Bwera, tiye tipite tikaphunzire (Dini) kuchokera kwa Ma Sahaabah (radhwiyallahu ‘anhum), pomwe ambiri a iwo akadalipo pakati pathu.”
Anandiyankha kuti, “Iwe Ibnu Abbaas! Ndikulumbira mwa Allah, ndikudabwa kuti ukuganiza kuti anthu adzafunika kukutchula (pa nkhani za dini) pomwe Ma Swahaabah akuluakuluwa alipo pakati pathu!”
Ngakhale kuti mnzakeyo ananena zimenezi, Abdullah bin Abbaas (radhwiyallahu ‘anhuma) sanataye mtima ndi chilichonse pa kusaka kwake ilm. Iye adati:
M’malo mwake, ndinapitiriza kufunafuna maphumziro ndipo ndinayamba kupita kwa Swahaabi aliyense (yemwe adamva hadith kuchokera kwa Rasulullah (Swallallahu ‘alaihi wasallam)).
Mwanjira imeneyi Abdullah bin Abbaas (radhwiyallahu ‘anhuma) anakwanitsa kusonkhanitsa ilm yambiri kuchokera kwa ma Swahaabah (radhwiyallahu ‘anhum). Anapitiriza kunena kuti:
Paulendo wanga opita kwa Sahaabi aliyense (radhwiyallahu ‘anhu), ndikapeza kuti akupuma, ndinkayala nsalu yanga pakhomo la nyumba yake ndikukhala pansi, ndikumuyembekezera kuti atuluke m’nyumba mwake. Nthawi zina, nkhope yanga ndi thupi langa lonse zinkada ndi fumbi ndikadikirira kunja kwa nyumba yake.
Komabe, izi sizinalepheretse Ibnu Abbaas kuti asiye kufunafuna maphunziro ndipo anapitiriza kukhala pansi pamwepo, akuyembekezera mwachidwi kutuluka kwa Sahaabi. Iye akunena kuti:
Swahaba akatuluka m’nyumba mwake momwe amapuma ndipo akandiona, ankati, “Oh msuweni wa Rasulullah (Swallallahu ‘alaihi wasallam)! N’chifukwa chiyani wabwera kwa ine? Ukanatumiza uthenga ondiitana, ndiye kuti ine ndikanabwera kwanu!” Ndikamva izi, ndinkayankha kuti, “Ayi! Ndikoyenera kuti ine ndibwere kwa inu (popeza ine ndine ophunzira ndipo inu ndi ustaad)!”
Abdullah bin Abbaas (radhwiyallahu ‘anhuma) anapitirizabe ntchito zake mpaka nthawi inafika pamene anthu anayamba kumutsatira kuti akaphunzire za dini. Iye anati:
Mnzanga wachi Ansaari adali adakali moyo mpaka nthawi imene anaona anthu akupindula ndi maphunziro anga (panthawiyo, anazindikira kuti zomwe ndinachita zinali zabwino), ndipo motero anati, “Munthu uyu watsimikizira yekha kuti ndi wanzeru kuposa ine.” (Mustadrak Haakim #363)
Alislaam Yeretsani mtima wanu potsatira chisilamu