Monthly Archives: July 2021

Kuwerenga Durood Usiku Ndi Usana Wa Tsiku La Jumuah (Lachisanu)

Sayyiduna Aws bin Aws (radhiyallahu anhu) akusimba kuti Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adati, “tsiku lopambana kwambiri ndi tsiku la Jumuah/lachisanu, kotero, Chulukitsani kundiwerengera durood tsiku limeneli popeza durood yanu imabweretsedwa kwa ine, masahabah adafunsa kuti, “durood yathu idzakufikani bwanji mukadzamwalira poti mafupa anu adzakhala ataola?” Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adayankha nati, “ndithudi Allah adailetsa nthaka kudya matupi a aneneri.”

Read More »

Zikhulupiliro zokhudza Allah – 2

6. Palibe chilichonse chofanana ndi Allah Taala mayina ake ndi mbiri zake. Iye ndiokwanilira ulemelero wake ndi mbiri zake, palibe chinachirichonse chofanana ndi Allah Ta'ala mphamvu kapena maonekedwe. Iye Allah Ta'ala alibe maonekedwe kapena mtundu ofanana ndicholengedwa chirichonse.

Read More »

Kulandila Satifiketi Yomasuridwa Ku Unaafiq Komanso Ku Moto Wa Jahannam

Sayyiduna Anas (radhiyallahu anhu) akusimba kuti, Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adati, “amene anganditumizire Durood kamodzi ngati malipiro ya Durood Allah adzamulipira munthu ameneyo sawabu ndikumuchitira chifundo ka 10, ndipo amene anganditumizire Durood kokwana ka 10 Allah adzamulipira munthu ameneyo sawabu zokwana 100, ndipo munthu amene anganditumizire Durood kokwana ka 100 Allah adzamulembera chiphaso pakati pa maso ake yommasura ku ukamberembere komanso ku chilango cha Jahannam, Ndiponso Allah adzamulemekeza munthu ameneyo pa tsiku la Qiyaamah pomudzutsa ndi gulu la anthu omwe adafera ku nkhondo”.

Read More »