1. Qiyamah idzachitika lachisanu. Amenewa adzakhala mapeto a dziko lapansi. Allah Tabaaraka wata’ala adzaliononga dziko lonse lapansili. Palibe amene akudziwa za tsiku limene dziko lidzathe.[1] 2. Allah Ta’ala adzamula Mngelo Israafeel (alaihis salaam) kuti ayimbe lipenga lomwe liri ndi maonekedwe onga nyanga manvekedwe alipengali adzayamba motsika ndipo azidzakwera pang’onopang’ono kufikira …
Read More »Zikhulupiliro Zokhudza Taqdeer (Chikonzero)
1. Taqdeer imatanthauza nzeru zobisika ndi zakuya zimene Allah alinazo, tanthauzo lina ndikuti Allah yekha ndi amene amadziwa chinachirichonse komanso zochitika mtsogolo, chabwino kapena choipa kaya zam’mbuyo zatsopano ngakhalenso za mtsogolo iye amazidziwa kale (kuti zochitika) zisanachitike.[1] 2. Allah Tabaaraka wataala adawapatsa anthu chisankho chochita zabwino kapena zoipa, pa zabwino …
Read More »Zikhulupiliro zokhudza mabukhu a Allah
5. Quran ndi bukhu lomaliza ndipo idavumbulutsidwa kwa Mtumiki (sallallahu alaih wasallam). Kudzera mukuvumbulutsidwa kwa Quran mabukhu ena onse adachotsedwa. 6. Allah Ta’ala adatenga udindo oyiteteza Quran kufikira tsiku la Qiyaamah, kotero, palibe kusintha kapena kupungula kulikonse komwe kungachitike ku bukhu limeneri. Tidakali mkati molongosora za mabukhu olemekezeka, Allah adapeleka …
Read More »Zikhulupiliro zokhudza mabukhu a Allah
1. Allah Ta’ala adavumbulutsa mabukhu osiyanasiyana kwa aneneri osiyanasiyana (ntendere wa Allah upite kwa iwo)kuti adzawaongole anthu. Tauzidwapo za mabukhu amenewa mu Quran yolemekezeka komanso mma hadith ndipo za mabukhu ena sitinadziwitsidwe.[1] 2. Timakhulupilira mabukhu onse amene adavumbulutsidwa ndi Allah kwa atumiki onse monga m’mene adavumbulutsidwira. Ndipo sitimakhulupilira m’mabukhu amene …
Read More »Zikhulupiliro Zokhudza Angelo
10. Angelo amene amamufunsa munthu mafunso m’manda maina awo ndi Munkar ndi Nakiir.[1] ndipo mafunso omwe amafunsa ndi awa: a) Mbuye wako ndindani? b) Ungatiuze chani chokhuza Muhammad sallallah alaih wasallam? c) Chipembedzo chako ndi chiti?[2] 11. Mnsilamu aliyense ali ndi M’ngelo komanso shaitaan, M’ngelo amamulimbikitsa munthuyo kuchita zabwino ndipo …
Read More »Zikhulupiliro Zokhudza Angelo
6. Mikaa’eel (alaihis salaam) ndi amene amayang’anira zachakudya ndi nvula, angelo ena amagwira ntchito pansi pake ndipo amayang’anira mitambo nyanja mitsinje ndi mphepo, amauzidwa zoti achite ndi Allah ndipo kenaka amapeleka uthenga kwa angelo ena omwe ali pambuyo pake. 7. Israafeel (alaihis salaam) amalamuridwa ndi Allah kuti achotse mizimu ya …
Read More »Zikhulupiliro Zokhudza Angelo
1. Angelo ndizolengedwa zomwe zilibe tchimo komanso adalengedwa kuchokera mukuwala, angelo samaoneka ndi maso athu, ndipo sii amuna kapena akazi. iwowa samadya kumwa kapena kugona monga amachitira munthu.[1] 2. Allah adawapatsa iwowa maudindo osiyanasiyana, amakwaniritsa lamulo lirilonse limene alamuridwa ndipo samanyozera malamulo a Allah.[2] 3. Sitimadziwa chiwelengero chenicheni cha Angelo …
Read More »Zikhulupiliro Zokhudza Atumiki a Mulungu alaihim Salaam
6. Kuchuluka kwa aneneri onse akudziwa ndi Allah yekha, timakhulupilira mwa atumiki onse angakhale ochuluka bwanji. 7. Monga ziliri kuti ndi chizindikiro cha utumiki, Allah amamulora mtumiki kuchita zodabwitsa zomwe zimatchedwa kuti Mu’ujizaat. Komano Tikuyenera kuzindikira kuti mtumiki ndi munthuso ndipo sangapange zodabwitsa mwa iye yekha, zimangochitika kudzera muchifuniro cha …
Read More »Zikhulupiliro Zokhudza Atumiki a Mulungu (alaihim Salaam)
1. Allah Ta’ala adatumiza atumiki osiyanasiyana kumayiko kuti awatsogolere anthu kunjira yowongoka.[1] 2. Mtumiki ankachita kusankhidwa ndi Allah Ta’ala. Allah Ta’ala ankasankha mwa akapolo ake amene wamufuna pantchito yotamandikayi. Utumiki sungapezeke ndimunthu aliyense kudzera mu ntchito zake ndikulimbikira kwake ayi (koma umachokera kwa Allah Taala).[2] 3. Mtumiki amene adapatsidwa bukhu …
Read More »Zikhulupiliro Zokhudza Mtumiki Wa Allah Muhammad (Sallallah alayhi wasallam)
5. Allah Ta’ala adamudalitsa Mtumiki (sallallah alayhi wasallam) ndi zabwino zapadera zimene Atumiki ndi aneneri a Mulungu sadapatsidwe. Mtumiki (salallah alayhi wasallama) akusimba kuti:
(Ndadalitsidwa ndi zinthu zisanu ndi chimodzi (6), zimene atumiki akale sadapatsidwepo, Ndadalitsidwa popatsidwa jawaamil al kalaam (Mau amodzi koma amatanthauzo ochuluka, mwachitsanzo Quran yolemekezeka komanso mahadith olemekezeka muli matanthauzo akuluakulu kuchokera mu mau ochepa),
Read More »