Pamene nthaka idzagwedezedwe kugwedezedwa kwenikweni. Ndipamene nthaka idzatuluse mitolo yake. ndipo munthu adzati; ´´Kodi nthaka Yatani? ``. Patsikulo limeneli nthaka idzaulula nkhani zake, Chifukwa choti Mbuye wake adzayiwuza kuti Itero. Patsiku limeneli anthu adzapita kumalo achiweruzo ali mmagulumagulu kukaonetsa ntchito zawo. Choncho amene angachite ntchito yabwino yolemera ngati njere yampiru adzaiwona. Ndipo amene angagwire ntchito yoipa yolemera ngati njere yampiru adzayiwona.
Read More »Monthly Archives: June 2022
Mngelo Amene Amayima pa Manda Odalitsika a Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) kuti Apereke Durood ya Ummah kwa Rasulullah Ummah
Sayyiduna Ammaar (radhiyallahu anhu) kuti Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adati, Allah adasankha mngelo amene amakhala pafupi ndi manda anga kuti adzindifikitsira Durood ya Ummah wanga ndipo adawazindikiritsa maina (ma hadith ena amanena kuti adapatsidwa mphamvu yozindikira mawu a anthu osiyanasiyana) zomwe zikutanthauza kuti palibe munthu amene angandiwelengere Durood tsiku lina lirilonse mpaka pa Qiyaamah pokhapokha mngeloyu amafikitsa kwa ine dzina la munthuyo komanso la bambo ake. (Amanena kuti) uyu ndi uje mwana uje amene wakuwerengerani Durood.
Read More »