Monthly Archives: June 2022

Ma sunna ndi miyambo ya nsembe ya kuzinga nyama (qurbaani) 2

6.Ndi sunnah osadya chinachirichonse kummawa kwa tsiku la Eidul Adha kufikira mpakana utabwerako ku swalah ya Eid.

Sayyiduna Buraidah (radhiyallahu anhu) akufotokoza kuti tsiku la Eidul Fitr Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) sankapita kukaswali Eid pokhapokha atadya kenakake, koma tsiku la Eidul Adha sankadya kalikonse pokhapokha atabwerako (kuchokera ku swalah ya Eidul Adha, akabwera ko koswali chinthu choyambilira kudya chinkakhala chiwindi cha nyama yomwe anazinga).

Read More »

Tafseer Ya Surah ‘Aadiyaat

Ndikulumbilira akavalo othamanga ali ndi phuma, Ndi otulutsa moto ku zikhotwa (pomenyetsa miyendo m'miyala), Ndi othira nkhondo adani m'mawa (dzuwa lisadatuluke), Ndi kuulutsa fumbi lambiri (kwa adani) nthawi imeneyo, Ndikulowelera mkatikati mwa adani. Ndithu munthu ali okanira mbuye wake (sathokoza Allah pa zimene amdalitsa nazo). Ndithudi iye pa zimenezi ndi mboni (yodzichitira yekha kupyolera mzochitachita zake). Ndipo ndithu iye ndi okonda chuma kwambiri (ndiponso ngwansulizo). Kodi sakudziwa zikadzatulutsidwa za mmanda, Ndikudzasonkhanitsidwa ndikuonekera poyera zomwe zidali m'mitima? Ndithu tsiku limenelo Mbuye wawo adzawadziwa kwambiri (ndikuwalongosolera zonse zochita zawo).

Read More »

Tembelero la Jibril (alaihis salaam) komanso Mtumiki Muhammad (sallallah alaih wasallam)

Hazrat Ka'b bin Ujra (radhiyallahu anhu) akulongosora nkhani iyi: tsiku lina lake Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adaitana maswahabah onse (radhiyallahu anhum) "tabwerani ku mimbar" titakhala moyandikira mimbari, Mtumiki sallallahu alaih wasallam adakwera thanthi (sitepe) yoyamba ndipo anatulutsa mawu onena kuti "Aameen" kenako adakweranso thanthi yachiwiri ndi kuyankhulanso kuti "Aameen" adakweranso yachitatu ndikunena mawu omwe aja onena kuti "Aameen", atamaliza kupereka Khutbah ndikutsika pa Mimbari paja tidamufunsa kuti, Oh Mthenga wa Allah, takumvani mukuyankhula mawu omwe sitinakumvenipo ndikale lonse mukuyankhula, (komwe ndikuyankhula mawu oti Aameen mpaka katatu pokwera mimbari)

Read More »

Ma sunna ndi miyambo ya nsembe ya kuzinga nyama(qurbaani)

1. Qurbaani ndi sunna yomwe ili yaikulu kwambiri komanso ubembedzi wapamwamba kwambiri mu Deen. Mu Quraan yotamandika, zatchuridwa mwapaderadera zokhudzana ndi Qurbaani, komanso maubwino ochuluka ndi kufunikira kwake zalimbikitsidwa mma hadeeth a olemekezeka Rasulullaah (sallallahu alaihi wasallam). Allah ta’ala wanena kuti      لَن يَنَالَ اللَّـهَ لُحُومُهَا وَلَا دِمَاؤُهَا وَلَـٰكِن …

Read More »

Masunnah Ochita Mumzikiti

4. Pitani kumzikiti modekha ndi mwa ulemu. musapite mukuthamanga.

Olemekezeka Abu Hurayrah (radhiyallah anhu) adati; ndinamumva Mtumiki wa Allah (sallallah alayhi wasallam) akunena kuti; Pamene iqqamah yachitidwa, musapite kukapemphera swala pamene mukuthamanga, Mmalo mwake, Mukuyenera kuyenda modekha ndi mwaulemu. Gawo laswalah limene mwalipeza ndi Imaam, pempherani. Ndipo gawo lomwe lakudutsani kwanirisani. (pamene imaam watsiriza swalah)

Read More »

Masunnah Ochita Mumzikiti

1. Valani moyenera pamene mukupita kumnzikiti

Allah ta’ala akuyankhula kuti: Oh Inu ana Aadam (alyhi salaam), zikongoleseni (valani zovala zozikongoletsera) pamene mukupemphera swalah munzikiti

Read More »

Angelo Akukhamukira ku Misonkhano ya Zikr

Hazrat Uqbah bin Aamir radhiyallahu anhu akusimba kuti Hazrat Rasulullah adati: “Ndithu, Misikiti ili ndi zikhomo (omwe ndi anthu odzipereka ku musjid, ochita ibaadah, monga ngati zikhomo zimakhomeredwa pansi). anthu oterowo, ngati atachoka ku Musjid, angelo amawasowa, ndipo ngati ali odwala, angelo amawachezetsa, ndipo angelo akawaona amawalandira, ndipo ngati angafunike, angelo amawathandiza kukwaniritsa zosowa zawo (Pamene ali (m’Msikiti kukumbukira Allah), kuwerenga kwa Duroud ndi zina zotero), Angelo amawazungulira kuyambira Kumiyendo yawo mpaka Kumwamba. Manja awo amene akulembera Duruud (yomwe ikuwerengedwa ndi anthu awa) Wonjezerani (zikr ndi Duruud) Allah akuonjezereni (zabwino)!” Pamene anthu awa ayamba kupanga zikr ya Allah, makomo akumwamba amatsekulidwa kwa iwo, mapemphelo awo amayankhidwa, anamwali aku Jannah akusuzumira pansi pawo, ndipo Allah amawaikira Chifundo Chake chapadera pokhapokha ngati Sachita china chilichonse, ndipo sakuchoka. Akachoka munzikiti , angelo amadzuka ndi kufunafuna Misonkhano ina ya zikr.

Read More »

Anthu amene asonkhana ndikuma werenga Durood akutidwa ndi chifundo cha Allah

Sayyiduna Anas (radhiyallahu anhu) akusimba kuti Mtumiki sallallahu alaih wasallam adati pali gulu la Angelo la Allah lomwe limazungulira dziko lonse lapansi kuyang'anaya yang'ana gulu la anthu omwe akupanga Dhikr, akakumana ndi gulu lachoncholo amalizungukira akatero amatumiza gulu lina la Angelo kupita kumwamba kukamudziwitsa Allah zomwe anthuwa akuchitazi, angelowa amauza Allah kuti "oh Allah, takumana ndi gulu la akapolo anu omwe akuutenga mtendere wanu kukhala chinthu chapamwamba kwambiri, a kuwerenga bukhu lanu, a kumuwerengera Durood Mtumiki wanu ndipo akukupemphani zosowa zawo za padziko lapansi komanso ku Aakhirah".Allah amayankha ndikunena kuti, akutileni mu chifundo changa"ndipo angelowa amachita chomwecho ndipo amapitiliza kunena mgululi muli uje ndi uje, amene ndi ochimwa kwambiri, komanso wangobwera kumapeto kwa zonse "Allah amayankha kuti, akutileni anthu onse mchifundo changa kuphatikizapo iyeyo popeza wina aliyense amene anakutiridwa mgululi alibe tsoka lirilonse komanso samanidwa chisomo changa."

Read More »