binary comment

Tafseer Ya Surah Zilzaal

بِسْمِ اللّٰهِ الرَّحْمٰنِ الرَّحِيمِ

إِذَا زُلْزِلَتِ الْأَرْضُ زِلْزَالَهَا ‎﴿١﴾‏ وَأَخْرَجَتِ الْأَرْضُ أَثْقَالَهَا ‎﴿٢﴾‏ وَقَالَ الْإِنسٰنُ مَا لَهَا ‎﴿٣﴾‏ يَوْمَئِذٍ تُحَدِّثُ أَخْبَارَهَا ‎﴿٤﴾ بأن ربك أوحى لها ﴿٥﴾ يَوْمَئِذٍ يَصْدُرُ ٱلنَّاسُ أَشْتَاتًا لِّيُرَوْا أَعْمٰلَهُمْ ‎﴿٦﴾ ‏فَمَن يَعْمَلْ مِثْقَالَ ذَرَّةٍ خَيْرًا يَرَهُۥ ‎﴿٧﴾‏ وَمَن يَعْمَلْ مِثْقَالَ ذَرَّةٍ شَرًّا يَرَهُۥ ‎﴿٨﴾‏

Pamene nthaka idzagwedezedwe kugwedezedwa kwenikweni. Ndipamene nthaka idzatuluse mitolo yake. ndipo munthu adzati; ´´Kodi nthaka Yatani? “. Patsikulo limeneli nthaka idzaulula nkhani zake, Chifukwa choti Mbuye wake adzayiwuza kuti Itero. Patsiku limeneli anthu adzapita kumalo achiweruzo ali mmagulumagulu kukaonetsa ntchito zawo. Choncho amene angachite ntchito yabwino yolemera ngati njere yampiru adzaiwona. Ndipo amene angagwire ntchito yoipa yolemera ngati njere yampiru adzayiwona.

إِذَا زُلْزِلَتِ الْأَرْضُ زِلْزَالَهَا ‎﴿١﴾‏ وَأَخْرَجَتِ الْأَرْضُ أَثْقَالَهَا ‎﴿٢﴾‏ وَقَالَ الْإِنسٰنُ مَا لَهَا ‎﴿٣﴾‏

Pamene nthaka idzagwedezedwe kugwedezedwa mwamphanvu. Ndipamene nthaka idzatuluse mitolo yake. Ndipo munthu adzati; Kodi nthaka yatani?”

Tsiku lachiweruzo nthaka idzayamba kunjenjemera ndikugwedezeka mwamphamvu. Ndipo idzatulutsa mitolo yomwe idali mkati mwake ndipo idzaonetsera poyera.

Mitolo yotulutsidwa kunja ndi nthaka, kutanthauza kuti anthu amene anaikidwa mmanda komanso miyala yamtengo wapatali monga golide siliva dayamondi ndi zinthu zina zonse zomwe zabisidwa munthaka. Miyala yamtengo wapatali imeneyi idzakhala balabala pamwamba panthaka opanda oyilabadila, poonetsera kusafunikira kwake kuzolengedwa zonse patsikuli.

Malingana ndi hadith yovomerezeka imene ikupezeka mubuku la Imaam Muslim (rahamahullah) “wokupha mnzake adzabwera nati `Kodi izi sizimene ndinamuphera nawo munthu wakutiwakuti? Odula ubale kamba kandalama adzabwera nati; Kodi si izi zimene ndinadula nawo ubale?

Mofananamo nthaka nawo idzaulula nkhani zake zonse zomwe zidachitikira panthakapo. Ndipo nthaka idzaulula ntchito zabwino komanso zoipa zimene anthu adagwira pamene anali panthakapo. Patsiku limeneli munthu adzawona nthaka ikutulutsa mitolo yake ndikupereka maumboni munthu modabwa adzafunsa nati ´: Kodi nthaka yatani?

يَوْمَئِذٍ تُحَدِّثُ أَخْبَارَهَا ‎﴿٤﴾

Patsiku limenelo idzaulula nkhani zake zonse. (zomwe zidachikira panthakapo)

Olemekezeka Abu Hurairah (radhiyallah anhu) akunena kuti Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adafotokoza ndime iyi ponena kuti; “Nthaka idzachitira umboni zokhudzana ndi ntchito zonse zomwe anthu adachita ali pamalo amenewo kaya ndimamuna kapena mkazi´´

يَوْمَئِذٍ يَصْدُرُ ٱلنَّاسُ أَشْتَاتًا لِّيُرَوْا أَعْمٰلَهُمْ ‎﴿٦﴾

Patsiku limenelo anthu adzabwera ali mmagulumagulu kukaonetsa zipatso za ntchito zawo.

Mdziko lino lapansi tikupeza kuti anthu onse abwino ndi oyipa  akukhalira limodzi namawonana popanda kugawikana.
Komabe patsiku limenelo Allah Ta’ala adzawagawa anthu kukhala magulu osiyanasiyana mofanana ndi ntchito. Anthu abwino adzakhala ndi gulu lawo ndipo anthu oipa adzakhala ndi gulu lawo. Ndipo kudzera mundondomeko imeneyi, Zochita za anthu zidzawonetsedwa kwa anthu ena.

‏فَمَن يَعْمَلْ مِثْقَالَ ذَرَّةٍ خَيْرًا يَرَهُۥ ‎﴿٧﴾‏ وَمَن يَعْمَلْ مِثْقَالَ ذَرَّةٍ شَرًّا يَرَهُۥ ‎﴿٨﴾

Amene angagwire ntchito yabwino ngakhale itakhala yolemera ngati njere yampiru adzayiwona. Ndipo amene angagwire ntchito yoipa yolemera ngati njere yampiru adzayiwona.

Ntchito ya munthu ngakhale itakhala yopepuka ngati njere yampiru adzaiwona (adzalandira malipiro ake). Choncho munthu asamaganizire ntchito iliyonse kukhala yopanda ntchito. Munthu aliyense akuyenera kulemekeza kantchito kalikonse kabwino komanso awope kantchito kalikonse koipa mosatengera kachepedwe kake. Ndipo ndizotheka kantchito kabwino komwe tikukachepetsako kangakhale komupatsa iyeyo chipulumutso ndi chipambano patsiku lachiweruzo. Chimodzimodzinso ndi zotheka kuti kantchito koipa kochepesetsa komwe timakapanga kangakhale njira yotipititsira kumavuto ndi chionongeko.

Check Also

Tafseer ya Surah Ikhlaas

بِسْمِ اللَّهِ الرَّحْمَٰنِ الرَّحِيمِ قُلْ هُوَ اللَّهُ أَحَدٌ ‎﴿١﴾‏ اللَّهُ الصَّمَدُ ‎﴿٢﴾‏ لَمْ يَلِدْ وَلَمْ يُولَدْ ‎﴿٣﴾‏ وَلَمْ يَكُن لَّهُ كُفُوًا …