Monthly Archives: May 2022

Ma ubwino omwe munthu yemwe amakaswalira kunzikiti amapeza

4. Kupitapita kumzikiti ndi njira yokhayo yomwe ingateteze Dini ya munthu.

Sayyiduna Mu’adh bin Jabal (radhiyallahu anhu) akusimba kuti Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adati, ndithudi satana ndi nkhandwe ya munthu (yomwe imansaka munthu kuti idye) monga m'mene nkhandwe ya ziweto imachitira yomwe imapezelera mbuzi yomwe ili yokhayokha, Pewani kukhala panokhanokha (kapena kutsata maganizo a okha) ndipo gwiritsitsani gulu la Ahlus-sunnah wal jamaa'ah ndikukhala limodzi ndi ummah komanso kulumikizana ndi mzikiti".

Read More »

Ma ubwino omwe munthu yemwe amakaswalira kunzikiti amapeza

1. Kupangira wudhu kunyumba komanso Kuyenda kupita kunzikiti ndi njira yokhululukidwa machimo ndikukwezedwa ulemelero.

Sayyiduna Abu Hurairah (radhiyallahu anhu) akufotokoza kuti Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adati: Munthu amene angapange wudhu kunyumba ndi Kuyenda wapansi kupita kunzikiti kuti akakwaniritse lamulo la Allah phanzi lirilonse lomwe angaponye amakhulukidwa machimo, ndipo phanzi lina lomwe angaponye adzakwezedwa ulemelero wake.

 

Read More »

Tafseer Ya Surah Bayyinah

Anthu okanira mwa eni bukhu komanso ma Mushrikiin (opembedza mafano) sadafune kusiyana ndi umbuli wawo komanso zikhalidwe zawo kufikira chisonyezo chidawafikira amene ndi Mtumiki wa Allah kwawerengera makalata oyeretsedwa. M'mene mukupezeka malamulo olongosoredwa mom eka bwino. Omwe adapatsidwa mabukhu sadalekane/sadasemphane ndikugawanikana kufikira pomwe zisonyezo zoonekera poyera zidawadzera. Ndipo adangolamuridwa kumpembedza Allah kuchokera pansi pa mtima kukupanga kupembedza kukhala kwa Allah yekha osamphatikiza ndi zina. Ndikuswali komanso kupeleka Zakaat nthawi zonse ndikuti imeneyo ndiye dini yoongoka komanso.

Read More »

Nkhani Yabwino Yochoka Kwa Allah Ta’ala Kwa Awo Amene Amawerenga Durood

Hazrat Abu Talhah (radhiyallahu anhu) akusimba kuti: Tsiku lina m'mawa, Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adabwera kwa ife ali wosangalala, mpaka chisangalalo chake chinawala kuchokera ku nkhope yake yodalitsika. Swahabah wina adafunsa: "E, Mtumiki (sallallahu alaih wasallam)! Taona kuti lero mwakondwa kwambiri. Chisangalalocho chikuwoneka bwino pa nkhope yanu yodalitsika."Mtumiki (sallallahu alaih wasallam ) adayankha: "Inde, Mtumiki wochokera kwa Mbuye wanga anabwera ndi uthenga wonena kuti: " Munthu Amene adzakuwerengere Durood mwa ummah wako kamodzi, Allah adzamulembera zabwino khumi, ndi kufafaniza ndi kukhululukira machimo ake okwana khumi, ndi kukweza udindo wake ku Jannah m’magawo khumi, ndikumuyankha Duruud yake mofanananso (ndiye kuti Allah amutumizira chifundo ndi madalitso khumi).

Read More »

Maubwino a Mzikiti

1 Mizikiti imatengedwa kuti ndimalo okondedwa kwambiri pamaso pa Allah. عن أبي هريرة رضي الله عنه أن رسول الله صلى الله عليه وسلم قال أحب البلاد إلى الله مساجدها وأبغض البلاد إلى الله أسواقها (صحيح مسلم، الرقم: 671) Sayyiduna Abu Hurairah (radhiyallahu anhu) akufotokoza kuti Mtumiki (Sallallahu alaih wasallam) adati: …

Read More »

Zofunika za Dunya ndi Aakhirah Zikwaniritsidwa chifukwa chowerenga Durood tsiku la Jumuah

Hazrat Anas bun Maalik (radhiyallahu ‘anhu) akusimba kuti Hazrat Mtumiki (sallallahu ‘alaihi wasallam) adati: “Iwo mwa inu amene amawerengera duruud kwambiri  mu dunya adzakhala oyandikira kwa ine pa tsiku la Qiyaamah nthawi iliyonse. Munthu amene? Munthu amene angandiwelengere Durood Usiku ndi usana wa lachisanuJumuah, Mulungu adzamkwaniritsilira zosoweka zake kwa zana limodzi, zofunika makumi asanu ndi awiri za Aakhirah ndi zofunika makumi atatu za dunya. Duruud ikatha kuwerengedwa Allah amaipeleka kwa mngelo yemwe adzaibweretse mmanda ndikadzamwalira ngati mmene mphatso imaperekedwera kwa inu, mngelo amandidziwitsa za muntbu amene wapanga duruud dzina lake komanso la bambo ake ndipo kenako ndimaisamala.

Read More »