Mngelo Amene Amayima pa Manda Odalitsika a Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) kuti Apereke Durood ya Ummah kwa Rasulullah Ummah

عن عمار بن ياسر رضي الله عنه قال قال رسول الله صلى الله عليه و سلم إن الله وكل بقبري ملكا أعطاه الله أسماء الخلائق وفي رواية أسماع الخلائق فلا يصلي علي أحد إلى يوم القيامة إلا أبلغني باسمه واسم أبيه هذا فلان بن فلان قد صلى عليك (رواه البزار كما في الترغيب والترهيب، الرقم: 2574، قال الهيثمي: رواه البزار وفيه ابن الحميري واسمه عمران يأتي الكلام عليه بعده … قال البخاري: لا يتابع على حديثه وقال صاحب الميزان: لا يعرف ونعيم بن ضمضم ضعفه بعضهم، وبقية رجاله رجال الصحيح كذا في مجمع الزوائد، الرقم: 17291)

Sayyiduna Ammaar (radhiyallahu anhu) kuti Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adati, Allah adasankha mngelo amene amakhala pafupi ndi manda anga kuti adzindifikitsira Durood ya Ummah wanga ndipo adawazindikiritsa maina (ma hadith ena amanena kuti adapatsidwa mphamvu yozindikira mawu a anthu osiyanasiyana) zomwe zikutanthauza kuti palibe munthu amene angandiwelengere Durood tsiku lina lirilonse mpaka pa Qiyaamah pokhapokha mngeloyu amafikitsa kwa ine dzina la munthuyo komanso la bambo ake. (Amanena kuti) uyu ndi uje mwana uje amene wakuwerengerani Durood. 

Ayyoob Sakhtiyaani (rahimahullah) ku Madinah Tayyibah

Sayyiduna Abdullah bin Mubaarak (rahimahullah) akufotokoza, ndinanva Imaam Abu Hanifah (rahimahullah) akunena kuti, nthawi yomwe Ayyoob Sakhtiyaani (rahimahullah) adali ku Madinah Tayyibah Ndidali pompo ndipo ndinkayang’ana m’mene ankapeleka salaam kwa Mtumiki (sallallahu alaih wasallam), ndidamuona atayang’anizana ndi mandawo nsana wake Utayang’ana ku Qiblah, adangoima opanda kutulutsako mawu mmalo mwake ankangolira.” (kulasatul Wafaa, 1/228)

Check Also

Kuwerenga Durood musanapange Dua

عن فضالة بن عبيد قال: بينا رسول الله صلى الله عليه وسلم قاعد إذ دخل …