Pankhondo ya Uhud Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adavulazidwa kwambiri ndi adani ndipo zitsulo za chipewa chake chodzitetezera pa nkhondo zinabaya pankhope yake yolemekezeka. Sayyiduna Abu Bakr Siddiq komanso Abu Ubaidah (Radhiyallahu anhuma) adathamangira kukamuthandizira Rasulullah (sallallahu alaih wasallam). Sayyiduna abu Ubaidah (radhiyallahu anhu) atafika pamene panali Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) …
Read More »Monthly Archives: October 2022
Tafseer Ya Surah Humazah
Tsoka kwa aliyense ochita miseche, wonyoza, wodziunjikira chuma ndikuchiwerengera! Akuganiza kuti chuma chake chidzamkhazika muyaya. Ayi! Ndithu, adzaponyedwa ku Hutwamah (kumoto waukali). Ndipo nchiyani chingakudziwitse kuti 'Hutamah' ndi chiyani? Ndi moto wa Allah woyatsidwa umene uzidzalowa m’mitima mwawo. (Motowo) udzatchingidwa ndi zipupa zitalizitali, ndi mizati yotambasulidwa (yotambasuka).
Read More »Masunnah Ochita Mumzikiti
31. Kupatula kupita kumzikiti kukapemphera, ngati kuli mtsonkhano omwe ukupangidwira mumzikiti, mukuyenera kupanga niya kuti mukupita kumzikiti kukaphunzira za Dini. Ngati wina angakwanitse kuphunzitsa dini choncho akuyenera kupanga niya kuti akubwera kumzikiti kukaphunzitsa dini. عن أبي هريرة رضي الله عنه قال سمعت رسول الله صلى الله عليه وسلم يقول من …
Read More »Kukhudzidwa Kwa Mzimayi Wachi Answaari Pa Nkhani Ya Nabi (Sallallahu Alaih Wasallam)
Ku nkhondo ya Uhud asilamu adavutika kwambiri ndi kugonja komanso asilamu ambiri adaphedwa. Pamene nkhani yokhudzana ndi asilikali akunkhondo aja inawapeza anthu a ku Madina, amayi adatuluka m’nyumba zawo kufuna kudziwa m’mene nkhondo imayendera. Pamene anthu ena adakasonkhana pa malo ena ake mzimayi m’modzi wachi Ansaar adafunsa modandaula kuti kodi …
Read More »