Ku nkhondo ya Uhud asilamu adavutika kwambiri ndi kugonja komanso asilamu ambiri adaphedwa. Pamene nkhani yokhudzana ndi asilikali akunkhondo aja inawapeza anthu a ku Madina, amayi adatuluka m’nyumba zawo kufuna kudziwa m’mene nkhondo imayendera.
Pamene anthu ena adakasonkhana pa malo ena ake mzimayi m’modzi wachi Ansaar adafunsa modandaula kuti kodi Nabi (sallallahu alaih wasallam) ali bwanji? Pamene mzimaiyu adauzidwa kuti bambo ake aphedwa adalankhula mawu oti “innaa lillaahi wa innaa ilaihi ra jiuun” ndipo mosaugwira mtima anabwerezanso funso lija lokhudzana ndi Nabi (sallallahu alaih wasallam).
Pamenepa adauzidwa kuti mamuna wake waphedwa, m’chimwene wake waphedwa komanso mwana wake wadulidwa dulidwa. Mosaugwira mtima, mzimayi uja anafunsabe za Nabi (sallallahu alaih wasallam).
Adauzidwa kuti Nabi (sallallahu alaih wasallam) alibwino bwino, komabe sanaupeze mtima, ndipo adakakamira kuti amuone Nabiiyo yekha ndi maso ake. Pamapeto pake maso ake atakhutitsidwa pomuona Nabi (sallallahu alaih wasallam), adayankhula kuti:
كل مصيبة بعدك جلل
O Nabi wa Allah! chifukwa cha madalitso okuonani inu nkhawa zonse zatha komanso mavuto onse atha.
Chikondi Cha Sahabah Wina Pa Mtumiki (Sallallahu Alaih Wasallama)
Munthu wina adafunsa Aliy (radhwiyallahu anhu) kuti, ndi Chikondi chochuluka bwanji chomwe masahabah adali nacho pa Mtumiki (sallallahu alaih wasallam)?
Aliy (Radhwiyallahu anhu) adayankha nati, ndikulumbira mwa Allah, Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adali okondeka kwambiri kwa ife kuposa munthu wachuma, ana athu ndi amayi athu, ndipo kukhala limodzi ndi iye kunali kokoma kuposa kumwa madzi ozizira pamene uli ndi ludzu kwambiri.