Sayyiduna Abu Ubaidah (radhiyallahu) anhu aluza mano ake

Pankhondo ya Uhud Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adavulazidwa kwambiri ndi adani ndipo zitsulo za chipewa chake chodzitetezera pa nkhondo zinabaya pankhope yake yolemekezeka.

Sayyiduna Abu Bakr Siddiq komanso Abu Ubaidah (Radhiyallahu anhuma) adathamangira kukamuthandizira Rasulullah (sallallahu alaih wasallam). Sayyiduna abu Ubaidah (radhiyallahu anhu) atafika pamene panali Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) anayamba kukoka zitsulo zomwe zinalowa mu mnofu mwake zija ndipo chidachoka chimodzi ndi mano. Choncho atachotsa chitsulo cha mbali imodzi dzino lolemekezeka limodzinso linachoka (la abu ubaida chifukwa ankaluma ndi mano ndi kumakoka). Mopanda kudzinena padzino limodzi lomwe lachokalo anagwiritsano ntchito mano ake pofuna kukoka chitsulo china chomwe chinattsalila chija. Ndipo anakwanitsa kulichotsa chomwechonso mukuteromu dzino linanso linagululuka.

Pamene zitsulo zija zidakokedwa ndikutulutsidwa kunja, magazi adayanba kutuluka kwambili kuchokera mu thupi la Mtumiki sallallahu alaih wasallam. Hazrat Malik Bin Sinaan amene ndi bambo awo a Hazrat Abu Saeedil Khudriyy (radhiyallahu anhu) adanyambita magazi a Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) ndi milomo yake. Zitatero Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adalankhula mawu onena kuti moto siungadzakhudze thupi lomwe magazi ake asakanikirana ndi magazi anga. (Musnad Abi Dawood At Tayalisi, #6)

Check Also

Abu Ubaidah (Radhwiyallahu ‘anhu) aluza mano ake pa nkhondo ya Uhud

Pankhondo ya Uhud, Rasulullah (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam) adamenyedwa koopsa ndi adani ndipo mano awiri …