Tafseer Ya Surah Humazah

وَيْلٌ لِّكُلِّ هُمَزَةٍ لُّمَزَةٍ ‎﴿١﴾‏ الَّذِى جَمَعَ مَالًا وَعَدَّدَهُۥ ‎﴿٢﴾‏ يَحْسَبُ أَنَّ مَالَهُ اَخْلَدَهُ ‎﴿٣﴾‏ كَلَّا لَيُنْبَذَنَّ فِى الْحُطَمَةِ ‎﴿٤﴾‏ وَمَآ اَدْرٰىكَ مَا الْحُطَمَةُ ‎﴿٥﴾‏ نَارُ اللّٰهِ ٱلْمُوقَدَةُ ‎﴿٦﴾‏ الَّتِى تَطَّلِعُ عَلَى الْأَفْـِٔدَةِ ‎﴿٧﴾‏ اِنَّهَا عَلَيْهِم مُّؤْصَدَةٌ ‎﴿٨﴾‏ فِى عَمَدٍ مُّمَدَّدَةٍ ‎﴿٩﴾‏

Tsoka kwa aliyense ochita miseche, wonyoza, wodziunjikira chuma ndikuchiwerengera! Akuganiza kuti chuma chake chidzamkhazika muyaya. Ayi! Ndithu, adzaponyedwa ku Hutwamah (kumoto waukali). Ndipo nchiyani chingakudziwitse kuti ‘Hutamah’ ndi chiyani? Ndi moto wa Allah woyatsidwa umene uzidzalowa m’mitima mwawo. (Motowo) udzatchingidwa ndi zipupa zitalizitali, ndi mizati yotambasulidwa (yotambasuka).

وَيْلٌ لِّكُلِّ هُمَزَةٍ لُّمَزَةٍ ‎﴿١﴾

Tsoka kwa aliyense ochita miseche, wonyoza!

Surayi ikuchenjeza za chilango choopsa chochita machimo akuluakulu atatu ndipo kenako yafotokoza ndi kulongosola m’mene chilango chaukalichi chilili. Machimo atatuwo ndi miseche, kunyoza ndi kudziunjikira chuma mwadyera.

Osakhulupirira ambiri ku Makka Mukarramah ankachita zoipa monga miseche, mijedo, kutukwana ndi kumunyoza Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa sallam). Amene ankachita zoipazi akudzudzulidwa m’ma ayah m’njira yochenjezanso Asilamu kuti asachitire ena zoipa.

M’surayi muli zoipa ziwiri zoyamba zomwe zikunenedwa: Humazah ndi Lumazah

Othirira ndemanga ambiri amavomereza kuti liwu loti “Humazah” lomwe lachokera ku liwu loti “Hamz” limatanthauza munthu amene amachita miseche kutanthauza kuti amalankhula zoipa za munthu kumbuyo kwake. Momwemonso, othirira ndemanga ambiri amavomereza kuti liwu loti “Lumazah” lomwe lachokera ku liwu lakuti “Lamz” limatanthauza munthu wonyoza kutanthauza kuti amalankhula zoipa za munthu pamaso pake.

Machimo onsewa ndi oipa mwamakharidwe komanso m’makhalidwe ndi akupha. Qur’aan Majeed ndi Sunnah zachenjeza mwamphamvu za machimo amenewa. Komabe, tikamaona mbali imodzi, kunena miseche n’koipa kwambiri kuposa kunyoza. Chifukwa chimene miseche imakhalira yoipitsitsa kwambiri n’chakuti pamene zoipa za munthu zanenedwa kumbuyo kwake, ndiye kuti wochitidwa misecheyo sakhalapo kuti adziteteze ndi kuthetseratu. Motero, uchimo umapitirira kuchitidwa mowonjezereka.

Komano, kunyoza, ngakhale kuti ndi tchimo loipa mwa iko kokha, n’kochepa kwambiri poyerekezera ndi miseche. Chifukwa chake n’chakuti wozunzidwayo alipo kuti adziteteze ndi kuthetsa kunyozedwa kumene akukumana nako. Komabe, tikaganizira mbali ina, ndiye kuti kunyoza n’koipa kwambiri kuposa miseche, popeza kunena zoipa za munthu pamaso pake n’kofanana ndi kumunyoza ndi kumuchititsa manyazi. Izi ndi zovulaza ndi zopweteka kwambiri pamakhalidwe ndi pagulu (poyerekeza ndi miseche yomwe siipweteka munthu popeza sakudziwa), choncho chilango chake ndi chokhwima kwambiri.

Kudzera mukukambirana za mavuto kapena zovuta za anthu, timaganiza kuti tikuchita zabwino ndi zopindulitsa, ndipo tikuthandiza anthu ammudzi. Komabe, choona chenicheni cha nkhaniyi ndi chakuti nthawi zambiri, zokambirana zimadutsa pa gheebah (miseche). Chifukwa chake, timachita tchimo popanda kuliwona ngati cholakwika.

Munthu akamakamba nthano, sazindikira komanso samvetsetsa kuti akuyambitsa kugawanikana pakati pa anthu. Anthu omwe ali ndi ubale komanso omwe mitima yawo ndi yogwirizana – kudzera m’nkhani zongopeka, mitima yawo imasweka ndipo maubale omwe akhalapo nthawi yayitali amasokonekera.

Mu Hadith, Nabiy (Swalla Allaahu ‘alayhi wa sallam) akuti:

وشرار عباد الله المشاؤون بالنميمة والمفرقون بين الأحبة الباغون البرآء العنت

Akapolo oipitsitsa a Allah Ta’ala ndi amene amakamba nkhani za anthu, kupanga udani pakati pa abwenzi ndi kufunafuna zolakwika za anthu osalakwa.

Hadith iyi ikunena kuti anthu oipitsitsa ndi anthu amene amakamba nthano ndi kupanga Fitnah.

Zolinga za anthu ambiri ndi zoipa ndipo amafunafuna njira zochitira chipongwe anthu osalakwa, kuthamangitsa opembedza kapena kunyoza anthu opanda chifukwa. Komabe, cholinga chawo sichina koma kubweretsa chisokonezo pakati pa anthu. Amadziwonetsera kukhala ofunira zabwino, kuyang’ana zabwino za deen, kotero kuti anthu amawawona ngati ndi anthu opembedza ndi oyera mtima. M’mene amawanyozera anthu ena zolinga zawo kumakhala kufuna kuwanyozetsa pokamba zoipa zawo iwo palibe yomwe ili miseche. Njira yawo imeneyi ndi yakuti amakumana nawo mwaulemu kwambiri, akumaoneka ngati opembedza kotero kuti anthu asamawaone ngati akuthetsa ubale. Panthawiyi, zotsatira za zochita zawo n’zakuti amathetsa mabanja ndi kuyambitsa kugawanikana pakati pa anthu.

الَّذِى جَمَعَ مَالًا وَعَدَّدَهُۥ ‎﴿٢﴾

Yemwe akuunjikira chuma ndikumachiwerengera

Cholakwika chachitatu chomwe chatchulidwa mu Aayah ndi cha munthu amene aunjika chuma ndikumachiwerengera. Kukonda mopambanitsa ndi kukhumbira chuma kumamulepheretsa munthu kugwiritsa ntchito chumacho mnjira zomwe Allah Ta’ala adalamula. Munthu amene aunjika chuma n’kumachiwerenga, amakhala ndi nkhawa nthawi zonse kuti awonjezere chuma chake.

Chenjezoli likugwira ntchito kwa munthu wolemera yemwe nthawi zonse amakhala wotanganidwa ndi kudzikundikira chuma chake popanda kutulutsa udindo wake kwa osauka kapena kwa Allah Ta’ala.

يَحْسَبُ أَنَّ مَالَهُ اَخْلَدَهُ ‎﴿٣﴾‏ كَلَّا لَيُنْبَذَنَّ فِى الْحُطَمَةِ ‎﴿٤﴾‏ وَمَآ اَدْرٰىكَ مَا الْحُطَمَةُ ‎﴿٥﴾‏ نَارُ اللّٰهِ ٱلْمُوقَدَةُ ‎﴿٦﴾‏ الَّتِى تَطَّلِعُ عَلَى الْأَفْـِٔدَةِ ‎﴿٧﴾

Akuganiza kuti chuma chake adzakhala nacho mpaka muyaya Ayi! Ndithu, adzaponyedwa ku Hutamah (kumoto waukali). Ndipo nchiyani chingakudziwitse kuti ‘Hutamah ndi chiyani? Ndi moto wa Mulungu woyatsidwa umene udzikalowa m’mitima mwawo. (Motowo) udzapangidwa kukhala Chotchinga pamwamba pawo (ndi kutsekeredwa pamwamba Pawo), ndi mizati yotambasulidwa.

Kaŵirikaŵiri, munthu akamapsya moto, choyamba amamva ululu m’ziŵalo zake zakunja, ndipo pamapeto pake amamva kupweteka m’ziŵalo zake zamkati ndi mtima. Komano, moto wa Jahannum ndi wamphamvu komanso woopsya kwambiri kotero kuti umakwera nthawi yomweyo kumtima. Kotero, mtima umene uli injeni ya thupi lonse, ndiye munthu angalingalire bwino lomwe ululu waukulu umene munthuyo angakhale nawo panthaŵiyo.

اِنَّهَا عَلَيْهِم مُّؤْصَدَةٌ ‎﴿٨﴾‏ فِى عَمَدٍ مُّمَدَّدَةٍ ‎﴿٩﴾‏

(Motowo) udzawatchinga ndikuwatsekera makomo mu nsalamira ndi zipilala zitalizitali ndipo zadzakwanitsa kugwedezeka M’menemo kapena kupulumuka

Mu Aayah imeneyi, Allah Ta’ala akufotokoza kuti moto mu Jahannum udzawatchinga pamwamba pawo ndi mizati yotambasuka. Choncho Adzazunguliridwa ndi moto ndi kutsekeredwa m’menemo momwemo kuti Sadzatha kuthawamo.

Check Also

Tafseer ya Surah Ikhlaas

بِسْمِ اللَّهِ الرَّحْمَٰنِ الرَّحِيمِ قُلْ هُوَ اللَّهُ أَحَدٌ ‎﴿١﴾‏ اللَّهُ الصَّمَدُ ‎﴿٢﴾‏ لَمْ يَلِدْ وَلَمْ يُولَدْ ‎﴿٣﴾‏ وَلَمْ يَكُن لَّهُ كُفُوًا …