Uphungu wa Abdullah bin Abbaas (radhiyallahu ‘anhuma)

Wahab bin Munabbih (rahimahullah) akunena kuti:

Olemekezeka Abdullah bin Abbaas (radhiyallahu ‘anhuma) atasanduka wakhungu (ku ukalamba wake), ndidamutsogolera ku Haram Sharif ku Makkah Mukarramah, komwe anamva gulu la anthu likukangana pakati pawo. Anandipempha kuti ndimulondolere kwa iwo.

Atafika kwa iwo, anawalonjera ndi mawu onena kuti “Assalaamu Alaikum”. Anamupempha kuti akhale pansi, koma iye anakana nati, “Kodi ndingakuuzeni za anthu omwe ali ndi ulemelero wapamwamba pamaso pa Allah Ta‘ala? Ndi anthu omwe mantha a Allah amachititsa kuti akhale chete, ngakhale kuti si ofooka kapena opusa. Ndipotu, amatha kulankhula bwino kwambiri ndipo ali ndi kumvetsetsa bwino. Komabe, zikr ya Allah Ta‘ala yawagonjetsa kwambiri ndipo salankhula zambiri. Akagwidwa ndi kukumbukira Allah Ta‘ala mozama, amafulumira kuchita zabwino. N’chifukwa chiyani mwadzipatura kwa anthu oterewa?”

Wahab bin Munabbih (rahimahullah) akuti, “Pambuyo pa uphunguwu, sindinaonenso gulu la anthu awiri atakhala pamodzi mu Haram Sharuf (ndikumachita zokambirana zokhudza apadziko lapansi).”

Zanenedwa kuti Ibnu Abbaas (radhwiyallahu ‘anhuma) ankalira kwambiri chifukwa choopa Allah Ta‘ala kotero kuti misozi yomwe inkatsika m’matsaya mwake inali inasiya zizindikiro pa iye.

Shaikh Moulana Muhammad Zakariyya (rahimahullah) adatchula nkhani yomwe ili mmusiyi:

Mu nkhaniyi, Abdullah bin Abbaas (radhwiyallahu ‘anhuma) wasonyeza njira yopepuka kwambiri yochitira zabwino. Uku ndikuganizira za ukulu wa Allah Ta‘ala. Ngati izi zingachitike, zimakhala zosavuta kuchita zinthu zina zonse zabwino moona mtima. Kodi n’kovuta kwambiri kuthera mphindi zochepa, mwa maola makumi awiri mphambu anayi a tsiku, kuganizira za ukulu wa Allah Ta‘ala?

(Fazaa’il-e-A’maal [Chingerezi] tsamba 43-44, [Chiurdu] tsamba 32-33)

Check Also

Ubale Wapafupi Umene Mu’aaz bin Jabal (radhwiyallahu ‘anhu) Anasangalala Nawo Ndi Rasulullah (swallallahu ‘alaihi wasallam)

Mu’aaz bin Jabal (radhwiyallahu ‘anhu) akunena kuti, “Nthawi ina, ndinali nditakhala kumbuyo kwa Rasulullah (sallallahu …