Tikayerekeza dini ya Chisilamu ndi zipembedzo zakale, timapeza kuti Chisilamu sichinangolongosora machimo ndi ntchito zoipa kuti ndi haraam, komanso chinafotokoza njira zomwe zimatsogolera ku uchimo ndi zoipa ngati haraam. Izi zidachitika kuti zimuteteze munthu kuti asagwere mu uchimo.
Taganizirani chitsanzo cha mowa chomwe chinali choloredwa m’zipembedzo zakale, koma chanenedwa kuti sichiloledwa mu Chisilamu. Chifukwa chomwe Chisilamu chimanenera kuti mowa ndi haraam ndichakuti zoipa za vinyo zimaposa zabwino zake, ndipo ndi njira yomwe imapangitsa munthu kuchita machimo ena ambiri.
Allah Talaa akufotokoza mu Quraan Majeed kuti:
يَسْئلُوْنَكَ عَنِ الْخَمْرِ وَالْمَيْسِرِ قُلْ فِيْهِمَا إِثْمٌ كَبِيرٌ وَمَنَافِعُ لِلنَّاسِ وَإثْمُهُمَا أَكْبَرُ مِنْ نَفْعِهِمَا
Akukufunsa (iwe Mtumiki Swallallahu alaihi wasallam) Za mowa ndi njuga.
Nena: “M’menemo muli masautso ndi uchimo waukulu ndi zina zothandiza kwa anthu, ndipo masautso ake ndi aakulu kuposa ubwino wake.”
Alislaam Yeretsani mtima wanu potsatira chisilamu