Durood Ndi Salawaat

Kufika Kwa Durood Ya Ummah Kwa Sayyiduna Rasulullaah (Sallallahu Alaih Wasallam)

Abu Hurairah (radhiyallahu anhu) akusimba kuti Rasulullah (sallallahu alaih wasallam) adanena kuti " nyumba zanu musazipange kukhala ngati ndi manda (zipangeni nyumba zanu kukhala za moyo popangilamo ntchito za bwino monga ngati swalah, kuwerenga Qur’aan majeed ndi zina zambiri. Choncho mukamatero nyumba zanu sizikhala ngati ndi manda kumene sikumachitikako ma aamaal abwino.) Ndipo manda anga musawatenge ngati ndi malo opangilapo zisangalalo, komanso mudziwerenga durood kwa ine, ndithudi mwa njira ina iliyonse Durood yo imandifika (kudzera mwa angelo) kuchokera kwina kuli konse komwe muli."

Read More »

Kupempha Chabwino Kuyambira Pa Tsinde Lake

Sayyiduna Abu Hurairah (radhiyallahu anhu) akufotokoza kuti, Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adati, "amene amawerenga Qur'an, amatamanda Allah Ta'ala, amawerenga Durood kumuwerengera Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) komanso amapempha chikhululuko kwa mbuye wake ndiye kuti wapempha zabwino kuyambira pa tsinde lake (kutanthauza kuti wachita ntchito zabwino zomwe ndi Chiyambi cha zabwino Zathu.

Read More »

Kukwaniritsidwa Zofuna Za Umoyo Uno Ndi Umoyo Otsiriza

Olemekezeka Habbaan bin Munqiz (Rahimahullah) akusimba kuti Sahaba wina adamufunsa Mtumiki (sallallahu alayhi wasallam) nati "O inu Mtumiki Wa Allah Kodi ndingapereke gawo limodzi m’magawo atatu (one third) a nthawi yanga imene ndiri nayo pokuwerengerani Durood? Mtumiki (sallallahu alayhi wasallam) adayankha nati, Inde ngati ungafune kutero, Ndiponso adafunsa nati kodi ndingaononge magawo awiri m’magawo atatu a nthawi yanga pokuwerengerani Durood? Rasulullah (sallallahu alayhi wasallam) adati inde ngati ungafune.Swahabayo adafunsanso nati kodi ndingaonongere nthawi yanga yonse pokuwerengerani durood? Mtumiki (sallallahu alayhi wasallam) adayankha nati" Ngati ungachite zimenezi, Allah Ta’ala adzakukwaniritsira chirichonse chomwe ukuchifuna kaya za duniya (dziko lapansi) kapena zaku Aakhirat.

Read More »

Kuthetsa Umphawi

Sayyiduna Samurah Suwaai (radhwiyallahu anhu), bambo a Jaabir radhwiyallahu anhu akufotokoza kuti, tsiku lina tidali pamodzi ndi Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) ndipo kudabwera munthu wina namufunsa Mtumiki (sallallahu alaihi wasallam) kuti, oh Mtumiki wa Allah (sallallahu alaihi wasallam), ndi ntchito (ibadah) iti yomwe ndi yokondedwa kwambiri pamaso pa Allah? 

Read More »

Kuyankhidwa Kwa Ma Duwa

Umar (radhwiyallahu anhu) akulongosora kuti: Duwa imakhala idakali pakati pa mitambo ndi nthaka (munlengalenga). Siimapititsidwa mpakana kumwamba ngati muduwamo simunawerengedwe Durood (kutanthauza kuti sipamakhala chitsimikizo cha kuyankhidwa kwa duwayo).

Read More »