وعن سمرة السوائي والد جابر رضي الله عنهما قال: كنا عند النبي – صلى الله عليه وسلم – إذ جاءه رجل فقال يا رسول الله ما أقرب الأعمال إلى الله قال صدق الحديث وأداء الأمانة، قلت يا رسول الله زدنا قال صلاة الليل وصوم الهواجر قلت يا رسول الله زدنا قال كثرة الذكر والصلاة علي تنفي الفقر قلت يا رسول الله زدنا قال من أم قوماً فليخفف فإن فيهم الكبير والعليل والصغير وذا الحاجة (معرفة الصحابة لأبي نعيم، الرقم: 3572، وسنده ضعيف كما في القول البديع صــ 278)
Sayyiduna Samurah Suwaai (radhwiyallahu anhu), bambo a Jaabir radhwiyallahu anhu akufotokoza kuti, tsiku lina tidali pamodzi ndi Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) ndipo kudabwera munthu wina namufunsa Mtumiki (sallallahu alaihi wasallam) kuti, oh Mtumiki wa Allah (sallallahu alaihi wasallam), ndi ntchito (ibadah) iti yomwe ndi yokondedwa kwambiri pamaso pa Allah? Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adayankha nati, kuyankhula zoona komanso kukwaniritsa malonjezo (kubweza katundu wa eni) ndidati, oh Mtumiki sallallahu alaih wasallam! tiuzeni malangizo ena (omwe angasangalatse Allah Ta’ala), Rasulullah (sallallahu alaih wasallam) adati, kudzukira usiku kuswali komanso kusala kudya masana m’nyengo yotentha, ndidapemphaso, oh Mtumiki (sallallahu alaih wasallam)! tiuzeninso malangizo ena, Rasulullah (sallallahu alaih wasallam) adati, kuchulukitsa kupanga zikr komanso kuwerenga Durood kawirikawiri zimathetsa umphawi, ndidapemphaso kachikena, oh Mtumiki (sallallahu alaih wasallam)! Tiuzeninso malangizo ena, Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adati, munthu yemwe akutsogolera anthu pa swalah (akupempheretsa) ayenera kufupikitsa swalah chifukwa choti, m’chigulugulumo muli nkhalamba, odwala, achinyamata komanso ena omwe ali ndi zochita zina (akufulumira).
Uthenga Wa Sayyiduna Sa’d (Radhwiyallahu Anhu) Kupita Kwa Asilamu Onse
Mkatikati mwa nkhondo ya Uhud, Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adafunsa, “kodi Sa’d Bin Rabee alikuti? Sindikudziwa m’mene alili. ’kenaka, m’modzi mwa masahabah adatumizidwa kuti akamuyang’ane Sa’d (radhwiyallahu anhu), adapita pa malo pomwe anthu ofera ku nkhondo adagonekedwa.
Adaitana mokuwa uku akutchula dzina la Sa’d kuti mwina adakali moyo. malo ena ake, mkatikati molengeza kuti watumidwa ndi Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) kuti amuyang’ane Sa’d (radhwiyallahu anhu), adamva mawu cha pansi pansi akuyankhulidwa mofooka kuchokera mbali ina, adatembenukira mbali imeneyo ndipo adampeza Sa’d bin Rabee atagona m’chigulugulu cha anthu omwalira ali pafupi kumwalira.
Sayyiduna Sa’d (radhwiyallahu anhu) adamveka kuyankhula mawu oti; mundipelekere salaam kwa Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) pamodzi ndi Uthenga uwu, “’O Mtumiki wa Allah! Allah akulipireni malipiro ochuluka kwambiri komanso okongora kudzera (mu Duwa yanga) mwa ine zimene Nneneri wina aliyense sanalipidweko kudzera mwa (duwa ya) omutsatira wake wina aliyense. ‘”
Kenaka adamuuza munthu amene adatumidwa kuti akamuyang’ane uja kuti, ukawadziwitse asilamu amnzanga kuti sadzakhululukidwa patsiku la Qiyamah ngati adani achisilamu angamufikire ndikumupha Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) (ndikupezeka kuti) iwowo asanamwalire, Pamapeto pa mawu amenewa, Sayyiduna Sa’d (radhwiyallahu anhu) adapuma mpweya wake omaliza ndikusiyana nalo dziko lino.
Ma sahabah adasonyeza kudzipereka kwawo pa Mtumiki (sallallahua alaih wasallam), uku atavulazidwa mabala uku akupuma mpweya wawo omaliza, adalibe nkhawa ina iliyonse palilime pawo ndipo adalibe maganizo ena koma kuganiza za m’mene Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adaliri, Allah atidalitse ndikutipatsa mtima omukonda Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) ngakhale chitakhala chochepa ngati njere ya mpilu chomwe ma sahabah adali nacho. (Muwatta Imaam Muhammad #1691)