Kupempha Chabwino Kuyambira Pa Tsinde Lake

عن أبي هريرة قال: قال رسول الله صلى الله عليه وسلم: من قرأ القرآن وحمد الرب وصلى على النبي صلى الله عليه وسلم واستغفر ربه فقد طلب الخير مكانه (شعب الإيمان، الرقم: ٢٠٨٤ ،وسنده ضعيف كما في القول البديع صـ ٢٨٠)

Sayyiduna Abu Hurairah (radhiyallahu anhu) akufotokoza kuti, Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adati, “amene amawerenga Qur’an, amatamanda Allah Ta’ala, amawerenga Durood kumuwerengera Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) komanso amapempha chikhululuko kwa mbuye wake ndiye kuti wapempha zabwino kuyambira pa tsinde lake (kutanthauza kuti wachita ntchito zabwino zomwe ndi Chiyambi cha zabwino Zathu.

Chikondi cha Sayyiduna Anas Bin Nadhr pa Mtumiki (sallallahu alaih Wasallam) komanso kuphedwa kwake pa Nkhondo ya Uhud

Pamene asilamu adayamba kugonjetsedwa pa nkhondo ya Uhud, mphekesera idafalikira paliponse kuti Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) waphedwa, mphekesera imeneyi idafooketsa masahabah ndikutaya chikhulupiliro mmitima mwawo.

Anas bin Nadhr (radhiyallahu anhu) adadzakumana ndi Umar komanso Talha pamodzi ndi gulu la maswahabah ena radhiyallahu anhum akuoneka okhumudwa. Iye adafunsa nati “ndichifukwa chani mukuoneka kuti ndiinu okhumudwa? Vuto ndi chani?” iwo adayankha nati; “Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) waphedwa.”

Sayyiduna Anas (radhiyallahu anhu) adayankha nati, “ngati zili choncho, ndiye ndindani angakonde kukhala ndi moyo ngati Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) wamwalira, tiyeni tipite chitsogolo tikamenye nkhondo ndi malupanga athu kuti nafenso tikakumane ndi okondedwa wathu Muhammad (sallallahu alaih wasallam). “Sipadadutse nthawi yaitali chiyankhulireni mawu amenewa koma adathamangira mchigulugulu cha adani ndikumenya nkhondo modzipereka mpakana adaphedwa ndikukha shahid.

Sayyiduna Anas (radhiyallahu anhu) adamukondetsetsa Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) kufikira kuti sadafune kuti akhale moyo padziko lapansi pano popanda Mtumiki (sallallahu alaih wasallam). (Dalailun Nubuwwah 245/3)

Check Also

Kuwerenga Durood musanapange Dua

عن فضالة بن عبيد قال: بينا رسول الله صلى الله عليه وسلم قاعد إذ دخل …