Zofuna Zathu Zokwana 100 Kukwaniritsidwa

عن جابر رضي الله عنه قال قال رسول الله صلى الله عليه وسلم من صلى علي في كل يوم مائة مرة قضى الله له مائة حاجة سبعين منها لآخرته وثالثين منها لدنياه (أخرجه ابن منده وقال الحافظ أبو موسى المديني: إنه غريب حسن، كذا في القول البديع صـ ٢٧٧)

Sayyiduna Jaabir (radhiyallahu anhu) akusimba kuti Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adati, “amene angawerenge Durood ka 100 tsiku lirilonse, Allah Ta’ala adzakwaniritsa zofuna zake zokwana 100, 70 adzalandira pa tsiku la Qiyamah ndipo 30 adzapatsidwa padziko pompano.

Kulemekezedwa Ndi Allah Ta’ala Chifukwa Chochulukitsa Kuwerenga Durood

Zanenedwa zokhudza Abul Abbas, Ahmed bin Mansour (rahimahullah) kuti, atamwalira, munthu wina ochokera M’dera lotchedwa Sheeraz adamulota sheikh ameneyu, kumalotoko, Ahmed bin Mansoor adaima ku Mihraab (kuchibula) munzikiti waukulu wa M’dera limeneli la Sheeraz, adakongoletsedwa ndizovala zokongora kumutu kuli chisoti cha ufumu chomwe chidali chokongoletsedwa ndi miyala ya ntengo wapatali.

Munthu uja adamufunsa sheikh uja kuti, Allah Ta’ala wakuchengeta bwanji? Iye adayankha nati, “Allah Ta’ala wandikhululukira machimo anga, wandilemekeza, wandinveka chisoti chaulemu chaku Jannah ndipo wandidalitsanso pondiuza kuti ndikalowa ku Jannah,” munthu uja adafusanso nati, ndi ntchito iti yomwe (yomwe udachita ndikupangitsa kuti) Allah akulemekeze chonchi? Ndipo iye adayankha kuti, zonsezi ndi chifukwa chochulukitsa kuwerenga Durood. (Al-Qawlul Badee Pg.259)

Check Also

Kuwerenga Durood musanapange Dua

عن فضالة بن عبيد قال: بينا رسول الله صلى الله عليه وسلم قاعد إذ دخل …