Kufika Kwa Durood Ya Ummah Kwa Sayyiduna Rasulullaah (Sallallahu Alaih Wasallam)

عن الحسن بن علي رضي الله عنهما أن رسول الله صلى الله عليه و سلم قال حيثما كنتم فصلوا علي فإن صلاتكم تبلغني (المعجم الكبير للطبراني، الرقم: ٢٧٢٩، وإسناده حسن كما في الترغيب والترهيب للمنذري، الرقم: ٢٥٧١)

Hazrat Hassan Bin Ali (radhiyallahu anhuma) akufotokoza kuti Rasulullah (sallallahu alaih wasallam) adanena kuti “Werengani durood kwa ine kwina kulikonse komwe mungakhale popeza durood yanuyo imafikitsidwa kwa ine (kudzera mwa angelo).

Olemekezeka Ummu Sulaim (radhiyallahu anha) Komanso Thukuta La Mtumiki (sallallahu alaih wasallam)

Bibi Ummu Sulaym (radhiyallahu anha) amene anali Mahram kwa Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adalongosora kuti tsiku lina Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adapita kunyumba kwake kuti akamuone ndipo mpaka adagona pang’no kuti apume (kugona kumeneku kumatchedwa kuti Qaylula) Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adayamba kutuluka thukuta.

Bibi Ummu Sulaym (radhiyallahu anha) akupitiliza kulongosora kuti adatenga botolo ndikuyamba kusonkhanitsa thukuta la Mtumiki (sallallahu alaih wasallam). Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) atadzuka adamufunsa Ummu Sulaym kuti akuchita chani, iye adanfotokozera Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) kuti akusonkhanitsa thukuta lake chifukwa panalibe china chirichonse chonunkhira bwino kuposa thukutali, Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adamulora iye kutero ndipo sadatsutsane nazo zimenezi. (Saheeh Muslim, #2332)

Check Also

Kuwerenga Durood musanapange Dua

عن فضالة بن عبيد قال: بينا رسول الله صلى الله عليه وسلم قاعد إذ دخل …