Zikhulupiliro zokhudza mabukhu a Allah

5. Quran ndi bukhu lomaliza ndipo idavumbulutsidwa kwa Mtumiki (sallallahu alaih wasallam). Kudzera mukuvumbulutsidwa kwa Quran mabukhu ena onse adachotsedwa.

6. Allah Ta’ala adatenga udindo oyiteteza Quran kufikira tsiku la Qiyaamah, kotero, palibe kusintha kapena kupungula kulikonse komwe kungachitike ku bukhu limeneri. Tidakali mkati molongosora za mabukhu olemekezeka, Allah adapeleka kwa anthu udindo oyang’anira mabukhuwa, komano mabukhuwa adatanthauzidwa mosayenera ndikusinthidwa.

7. Quran yolemekezeka idavumbulutsidwa kwa zaka 23. Ma Ayaa ena ochokera mu masurah osiyanasiyana adavumbulutsidwa nthawi zosiyana. Allah adamulamula Jibril (alaihis salaam) kuti amuuze Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) kuti ayaa iyi malo ake ndi surah yanji komanso masurawo ayikidwe mu ndondomeko yanji.


[٥] ثم الكتب قد نسخت بالقران تلاوتها وكتابتها وبعض أحكامها ( شرح العقائد النسفية صــ 168)

[٦] اِنَّا نَحْنُ نَزَّلْنَا الذِّكْرَ وَاِنَّا لَهۥ لَحٰفِظُوْنَ (سورة الحجر: ٩)

[٧] (وقرآنا فرقناه) أما قراءة من قرأ بالتخفيف فمعناه فصلناه من اللوح المحفوظ إلى بيت العزة من السماء الدنيا ثم نزل مفرقا منجما على الوقائع إلى رسول الله صلى الله عليه وسلم في ثلاث وعشرين سنة قاله عكرمة عن ابن عباس (تفسير ابن كثير 5/127)

Check Also

Zikhulupiliro Zokhudza Angelo

10. Angelo amene amamufunsa munthu mafunso m’manda maina awo ndi Munkar ndi Nakiir.[1] ndipo mafunso …