Ubwino wa Muadhin

Adhaan ndi chimodzi mwazizindikiro za chisilamu, chisilamu chimalemekeza kwambiri anthu amene amapanga Adhaan, kuwaitanira anthu kuti adzaswali.Tsiku lachiweluzo anthu adzawasilira anthu amene ankachita adhaan padziko lino lapansi chifukwa cha ulemelero umene anthuwa adzakhale nawo. Ma hadith ochuluka alongosora za maubwino a muadhin ndi zabwino zimene akalandire patsikuli.

1. Muadhin adzakhala pa ulemelero wapamwamba patsiku la chiweluzo.

عن معاوية رضي الله عنه قال سمعت رسول الله صلى الله عليه وسلم يقول المؤذنون أطول الناس أعناقا يوم القيامة (صحيح مسلم، الرقم: 387)

Sayyiduna Mu’aawiyah (radhiyallahu anhu akusimba kuti, ndidanva Mtumiki wa Allah madalitso ndi ntendere zipite kwa iye akunena kuti, opanga Adhaan adzakhala ndi makosi ataliatali patsiku la Qiyaamah.

Mu hadith imeneyi tanthauzo loti makosi ataliatali sikutalika komwe tikukudziwaku, komano tanthauzo lake ndiloti adzakhala pa ulemelero wapamwamba kwambiri.

2. Ma muadhin adzakhala m’mapiri a pelefyum onukhira kwabasi patsiku la Qiyaamah.

 عن عبد الله بن عمر رضي الله عنهما قال قال رسول الله صلى الله عليه وسلم ثلاثة على كثبان المسك أراه قال يوم القيامة يغبطهم الأولون والآخرون رجل ينادي بالصلوات الخمس في كل يوم وليلة ورجل يؤم قوما وهم به راضون وعبد أدى حق الله وحق مواليه (سنن الترمذي، الرقم: 2566, وقال: هذا حديث حسن غريب)

Sayyiduna Abdullah(radhiyallahu anhu akufotokoza kuti Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adati,“Anthu atatu adzakhala pa mapiri a musk (patsiku la Qiyaamah) anthu akale ndi atsopano adzachitira nsanje chifukwa cha ulemelero wawo, munthu oyamba ndi amene ankachita adhaan kuwaitana anthu kuti abwere kuswala nthawi chipindi china chirichonse. Munthu wachiwiri ndi amene adatsogolera anthu pa swalah ndipo anthuwo adasangalatsidwa ndi utsogoleri wake (kutanthauza kuti adakwaniritsa malamulo onse apaswalah, ndipo omaliza ndi munthu amene adali kapolo ndipo kuphatikiza pa ukapolo wakewo adakwaniritsanso malamulo a Allah Tabaaraka wata’ala”

Check Also

Mawu A Iqaamah Komanso Njira Ya Sunnat Yopangira Iqaamah

1. Mawu a Iqaamah ndichimodzimodzi ndi azaana. Koma popanga iqaamah mukuyenera kunena kamodzikamodzi kupatula mawu …