Nkhani Yokhudza Kulowa Chisilamu Kwa Sayyiduna Wahshi Radhwiyallahu Anhu

Pankhondo ya Uhud, chimodzi mwa zowawa zowawitsa zomwe zidamuchitikira Rasulullah swallallahu alaihi wasallam kudali kuphedwa kwa amalume ake okondedwa Sayyiduna Hamzah radhwiyallahu anhu Amene adamupha Hamzah sanali wina koma Wahshi bun Harb

Nthawi imeneyo ndikuti asadakhale nsilamu, koma Allah Talaa pambuyo pake adamdalitsa ndi Imaan ndi ulemelero okhala Sahaabi.

Nkhani yokhudza kuvomera kwake Chisilamu ili motere:

Pambuyo poti Allah Talaa adamudalitsa Mtumiki Swallallahu alaihi wasallam ndi ma Swahaabah radhwiyallahu anhum pogonjetsa Makka Mukarramah, Hazrat Wahُshiadathawira ku Taa’if, poopa kuti Asilamu angamugwire ndikumupha ngati kubwezera imfa ya Hamzah radhwiyallahu anhu.

Pambuyo pake anthu aku Taa’if atafuna kulowa chisilamu, adatumiza nthumwi kwa Mtumiki Swallallahu alaihi.

Nthawi imeneyo Wahshi radhwiyallahu anhu nayenso adatsagana ndi nthumwi imeneyi nadzafika ku Makka Mukarramah. Atadza kwa Mtumiki Swallallahu alaihi wasallam Rasulullah swallallahu alaihi adamfunsa: “Kodi ndiwe Wahshi?” Hazrat Wahshi radhwiyallahu anhu anayankha “Inde, ndine Wahshi.”

Kenako Mtumiki Swallallahu alaihi wasallam adati: “Kodi ndiwe amene udapha Hamzah?

Hazrat Wahshi adayankha nati, “Inde, nkhani (yokhudza ine kupha amalume anu) ili yomwemo momwe mudamvera (ndine amene ndidapha amalume anu).”

Ngakhale Wahshi radhwiyallahu anhu adapha amalume ake Hazrat Hamzah radhwiyallahu anhu Rasulullah swallallahu alaihi wasallam adali ndi nkhawabe za chipulumutso chake. Nkhawa yaikulu imeneyi idali yochokera mu chikondi chakuya chimene Mtumiki Swallallahu alaihi wasallam anali nacho pa Ummati wake.

Choncho, Rasulullah swallallahu alaihi wasallam nthawi yomweyo adamuitanira Hazrat Wahshi radhwiyallahu anhu kuti alowe m’Chisilamu………..

Check Also

Makolo Kutsogolera Mwa Chitsanzo

Rasulullah (swallallahu alaihi wasallam) anali olemekezeka kwambiri pa zolengedwa za Allah, Allah adamusankha kukhala Mtumiki …