
Nthawi ina, Rasullullah (Swallallahu alaihi wasallam) anabwera ku fuko la Bani Zafar (fuko lachi Ansaar). Ali pa mimbar akulankhula nawo, anamuuza Abdullah bin Mas’ood (radhwiyallahu ‘anhu), kuti, “Ndiwerengere Quraan.”
Modzichepetsa kwambiri, Abdullah bin Mas’uud (radhwiyallahu ‘anhu) anauza Rasulullah (Swallallahu alaihi wasallam), “Eh Mtumiki wa Allah, kodi ndikuwerengereni kumachita kuti Quraan Majeed idavumbulutsidwa kwa inu?”
Rasullullah (Sallallahu alaihi wasallam) adati, “Ndikufuna kumva ikuwerengedwa kuchokera kwa wina osati ine mwini.”
Kenako Abdullah bin Mas’uud (Radhiyallahu ‘anhu) anayamba kuwerenga Surah Nisaa, Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wa sallam) ankamvetsera mwachidwi kuwerenga kwake. atafika ayah 41 yomwe ndi:
فَكَيْفَ إِذَا جِئْنَا مِن كُلِّ أُمَّةٍ بِشَهِيدٍ وَجِئْنَا بِكَ عَلَىٰ هَٰؤُلَاءِ شَهِيدًا ﴿٤١﴾
Nanga zidzakhala bwanji tikadzabweretsa Mboni pa mbadwo ulionse ndikukubweretsa Iwe (Mneneri Muhammad (Swallallahu alaihiwasallam) kuti ukhale Mboni pa mbadwo uwu.
Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wa sallam) adati kwa iye: “Utha kuimikira kuwerenga tsopano.”
Abdullah bin Mas’uud (radhwiya Allahu ‘anhu) atamuyang’ana Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wa sallam), adapeza kuti maso a Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wa sallam) akutuluka misozi (chifukwa cha ulemerero ndi udindo wapamwamba wa Allah) omwe Allah adzamudalitse nawo pa tsiku la Qiyaamah monga momwe yanenera ndime ya pamwambayi). (Swahiyh Bukhaariy #5055, Fathul Baari 99/9)
Alislaam Yeretsani mtima wanu potsatira chisilamu