Sunnats Ndi Aadaab Pa Kumwa 2

7. Osamwera mbali yomwe ndi yodulidwa kapena yosweka ya chikho, chifukwa ndizotheka kuti mutha kuvulala.

Olemekezeka Abu Sa’eed Khudri (radhwiyallahu anhu) akusimba kuti Rasulullah (swallallahu alaihi wasallam) adamuletsa munthu wina kumwera mbali ya chikho yophwanyika kapena kusweka.

8. Musauzire m’pweya m’chiwiya.

Sayyiduna Ibnu Abbaas (radhwiyallahu anhuma) akunena kuti Rasulullah (swallallahu alaihi wasallam) analetsa kupumira mu chiwiya kapena kuuziramo.

9. Ngati chakumwa ndi chogawana ndi anthu ochepa, ndiye kuti munthu oyamba akamwa, ayenera kupereka chakumwacho kwa amene ali kudzanja lake lamanja.

Sayyiduna Anas (radhwiyallahu anhu) adanena kuti nthawi ina, mkaka wina osakanikirana ndi madzi pang’ono (ngati kuziziziritsa) udaperekedwa kwa Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam). Nthawi imeneyo, Beduuin adakhala mbali ya kumanja kwa Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam). Pambuyo pa Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) adapereka chiwiyacho kwa Beduin kuti amwe ndipo adati: “Apatsidwe kaye amene ali kudzanja lamanja, ndipo pambuyo pake amene ali kudzanja lake lamanja.

10. Nenani dua iyi mukatsiriza kumwa madzi:

الْحَمْدُ لِلَّهِ الَّذِي سَقَانَا عَذْبًا فُرَاتا بِرَحْمَتِهِ وَلَمْ يَجْعَلْهُ مِلْحًا أُجَاجا بِرَحْمَتِهَ

Kuyamikidwa konse nkwa Mulungu Talaa yemwe watipatsa madzi akumwa osangalatsa ndi chisomo Chake, ndipo sadawapange kukhala amchere ndi owawa chifukwa cha machimo athu.

11. Nenani dua iyi mukatha kumwa mkaka:

اللَّهُمَّ بَارِكْ لَنَا فِيْهِ وَزِدْنَا مِنْهُ

Oh, Allah Talaa, tipatseni barakah mumkakawu ndipo tidalitseni ndi zambiri.

Check Also

Ma Dua Onena Ukamaliza Kudya

Dua Yoyamba اَلْحَمْدُ لِله الَّذِي أَطْعَمَنَا وَسَقَانَا وَجَعَلَنَا مُسْلِمِينَ Kuyamikidwa konse ndi kwa Allah amene …