Kuti dziko liziyenda bwino komanso mogwirizana, ndikofunikira kuti munthu aliyense alemekeze ufulu wa anthu ena.
Ngati ufulu wa anthu siulemekezedwa ndi kukwaniritsidwa, ndiye kuti chisokonezo ndi mikangano zidzafalikira padziko lonse lapansi. Kuba ndi kulanda chuma kudzakhala paliponse ndipo kuponderezana ndi kuphwanya malamulo kudzakhala chinthu chotchuka kwambiri.
Anthu adzapondereza ufulu wa ofooka ndi okalamba, akazi ndi ana, ndikuwagwiritsa ntchito chifukwa sangakwanitse kudziteteza okha ndikuteteza ufulu wawo.
Pa chifukwa chimenechi shari’ah chafotokoza ufulu wa anthu komanso momwe ufulu wawo uyenera kulemekezedwera.
Lamulo la Quraan Majiid Lokhudza Anansi
Mu Quraan Majiid, Allah Taala akuti:
“Onetsani kukoma mtima pa makolo, achibale, ana amasiye, osowa, mnansi wapafupi, mnansi wakutali ndi mnzanu yemwe mukukhala naye pafupi “
Mu ndime yomwe ili pamwambayi, ufulu wa anthu omwe Allah akukamba ndi ufulu wa anansi. Mmahadith olemekezeka Mtumiki sawallhu alayhi wassallam watsindika kwambiri zolemekeza ndi kusamala ma ufulu a neba.
Mtumiki sawallhu alayhi wassallam adati:
“Okhulupirira weniweni samadya mpaka kukhuta pomwe akudziwa kuti mnansi wake ali ndi njala.”
Mtumiki swallallahu alaihi wasallam Kufotokoza Ufulu wa Anthu oyandikana nawo nyumba.
Hazrat Mu’aawiyah bin Haydah radhwiyallahu anhu adanena kuti nthawi ina adamufunsa Mtumiki swallallahu alaihi wasallam”Kodi maufulu a munthu oyandikana naye nyumba ndi otani Oh Rasulullah swallallahu alaihi wasallam.
Rasulullah (swallallahu alaihi wasallam) anayankha kuti, “Uyenera kumuyendera (ndi kumusonyezera chidwi) akadwala, kupita ku maliro ake akamwalira, kumuthandiza ndi ngongole ngati wakudandaulira, ndipo ngati agwa m’mavuto chifukwa cha umphawi, uyenera kubisa umphawi wake (kudzera mu kumuthandiza mwanjira yoti wina asadziwe).
“Ngati zikumuyendera, uyenera kumuyamikira, ndipo ngati tsoka limugwera, uyenera kumumvera chisoni.””Komanso, usakweze nyumba yako kuposa yake, popeza kutero kudzachititsa kuti mpweya wabwino m’nyumba mwake usamafike.
“Musamumvetse kuwawa kulikonse chifukwa cha fungo lochokera ku ziwiya zanu (pamene mukuphika mwachitsanzo, chifukwa chakuti sangakwanitse kugula chakudya chamtunduwu, usamusowetse chifukwa cha umphawi wake polora fungo la chakudya chanu kumufikira ngati kukhala ndi braai) pokhapokha ngati muli ndi maganizo omupatsako chakudya china ndikugawana naye.”
Chenjezo Lochokera Mmahadith Kwa Iwo Omwe Amachitira Maneba Awo Zoipa
Monga momwe ziliri kuti mahadith amalimbikitsa kwambiri za kukwaniritsa ufulu wa neba, momwemonso pali chenjezo ndi malangizo amphamvu omwe amanenedwa okhudza kuzunza neba.
Olemekezeka Abu Hurairah (radhwiyallahu anhu) wafotokoza kuti Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam) adati: “Amene amakhulupirira mwa Allah Talaa ndi tsiku la Qiyaamah asabweretse vuto lirilonse kwa neba wake.”
Mu Hadith ina, zanenedwanso kuti Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam) anabwereza katatu mawu awa: “Ndikulumbirira m’dzina la Allah, munthu sangakhale okhulupirira mwangwiro.”
Sahaabi adafunsa: “Eh Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam)! Kodi mukutanthauza munthu uti?” Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam) adati: “Amene mnzake satetezedwa ku zoipa zake.”
Ulendo wina munthu adadza kwa Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam) nati: “Eh Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam)!pali mzimayi wina yemwe ndi odziwika kwambiri ndi kuswali kupereka chopereka komanso amasala swarm ya sunnah, koma vuto lake ndi munthu yemwe amachitira zoipa aneba ake.”
Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam) adati: ” akalowa kumoto (adzalangidwa ndi Allah Talaa chifukwa chochitira zoipa anansi ake).”
Kenako munthuyo adati: “Eh Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam)! Ndithu, ndikudziwa za mkazi wina yemwe samaswali swalah za nafl zochuluka, ndipo samachulukitsa kusalah swaum za sunnah, ndiponso samapereka sadaqa zambiri, koma amagawira aneba ake tchizi ndipo samapereka mavuto alionse kwa neba wake(amalemekeza ufulu wa aneba ake).
Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam) adati: “Iye adzakalowa ku Jannah (chifukwa cha kupemphera). kuchitira zabwino anansi ake, adzalipidwa ndi Jannah).
Kuchokera mu hadith yomwe ili pamwambayi, tikumvetsa kuti Chisilamu chapereka ufulu kwa anansi komanso kufunikira kwake.
Pa chifukwa chimenechi, tiyenera kuyesetsa, nthawi zonse, kukwaniritsa ufulu wa aneba athu ndikuonetsetsa kuti sitikuwapangitsa kukhala osowa ntendere kapena kuzunzika nthawi iliyonse.
Allah Talaa atidalitse ndi tawfeeq yokwaniritsa ufulu wa maneba athu komanso ma ufulu ena omwe tikuyenera kukwaniritsa kwa zolengedwa za Allah Talaa.
Alislaam Yeretsani mtima wanu potsatira chisilamu