1)Musanamwe, Nenani dzina la Allah powerenga
بِسْمِ الله
M’dzina la Allah.
2) Imwani ndi dzanja lamanja.
Olemekezeka Ibnu Umar radhwiyallah anhuma akunena kuti Rasulullah adati, “Aliyense wa inu akamayamba kudya, ayenera kudyera dzanja lake lamanja, ndipo akamamwa, ayenera kumwera dzanja lake lamanja, pakuti Shaitaan amadya ndi dzanja lake lamanzere ndi kumwa ndi dzanja lake lamanzere.
3) Ndi bwino osamwera m’botolo kapena chiwiya chomwe sichikuoneka mkati mwake chifukwa chakuti n’kutheka kuti mukhoza kukhala chinthu changozi mkati mwa botolo kapena chiwiya (ngati zilombo). M’malo mwake pakuyenera kuthira mkapu zomwe zili m’botolozo kenako ndikumwa.
4. Ndi bwino kukhala pansi ndikumwa. Komabe, ngati ndi madzi a Zam Zam kapena madzi omwe amatsalira mchitini pambuyo pa wudhu, ndiye kuti ukhoza kumwa chiimire.
5. Mukamamwa, musameze zakumwa zonse zomwe zili mkapu nthawi imodzi, chifukwa izi zingaononge thupi lanu. M’malo mwake, muyenera kumwa katatu modukizadukiza. Ngati zili mkapuzo ndi zochepa kwambiri moti munthu angathe kumwa kamodzi kapena kawiri, ndizoloredwa kumwa katatu.
Olemekezeka Ibnu Abbaas radhwiyallah anhuma akufotokoza kuti Rasulullah swallallahu alaihi wasallam adati: “Musamwe mwakamodzi ngati ngamira, koma Imwani modukiza ngati kawiri kapena atatu, ndipo tchulani dzina la Allah mukayamba kumwa, ndipo mtamandeni Allah mukamaliza kumwa.”
6. Pamene mukumwa, muthokozeni Allah chifukwa cha chakumwa chimene wakupatsani ponena mawu oti “Alhamdulillah”.
Olemekezeka Anas radhwiyallahu anhu akusinba kuti Hazrat Rasulullah swallallahu alaihi wasallam adati: “Ndithu Allah Talaa amasangalala ndi kapolo amene amadya cha chakudya chochepa, kapena kumwa madzi ochepa, ndi kumutamanda Allah (kusonyeza kuyamika) pa zimenezo.
Alislaam Yeretsani mtima wanu potsatira chisilamu